Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Mu gawo la nthambi yathu kuno ku Malawi, tsopano tili ndi abale okwana 265 amene anaphunzira Sukulu Yophunzitsa Utumiki ku Zambia ndiponso ku Malawi. Ndipotu anthu 218 mwa amenewa ndi oti anachita maphunziro awo ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki ya ku Malawi konkuno. Mwa anthu amenewa, 97 akutumikira ngati apainiya apadera ndipo 39 akutumikira monga oyendayenda.