Zochitika mu Utumiki Wakumunda
N’zosangalatsa kwambiri kuona kuti Yehova akutidalitsa chifukwa cha khama limene tikuchita posonkhanitsa anthu okhala ngati nkhosa m’gawo lathu. Kwa nthawi yoyamba, m’mwezi wa December 2010, ofalitsa onse tinakwana 79,157. Tiyeni tipitirize kulalikira mwakhama kuti tipeze anthu ambiri amene akufunafuna choonadi ndiponso kuti tiwathandiza mapeto a nthawi ino asanafike.—Mat. 28:19, 20.