Zilengezo
◼ Mabuku ogawira m’mwezi wa July ndi August: Gawirani kabuku kalikonse ka masamba 32 kamene anthu angachite nako chidwi m’gawo lanu, monga: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dikirani!, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Sangalalani Ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! ndi kakuti, “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” September: Gawirani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo pa ulendo woyamba. October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukapeza anthu achidwi, agawireni kapepala kakuti, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo.