Zochitika mu Utumiki Wakumunda
M’mwezi wa February chaka chino, tinachititsa maphunziro a Baibulo okwana 86,680. Umenewu ndi umboni wakuti pali anthu ambiri amene akuusa moyo ndi kubuula chifukwa cha zonyansa zonse zimene zikuchitika m’dzikoli masiku ano. (Ezek. 9:4) Tikufunanso kuthokoza aliyense chifukwa takhala tikulandira malipoti pa nthawi yake kwa miyezi itatu yapitayi. Tipezerepo mwayi wodziwitsa akulu kuti muziyesetsa kutumiza malipoti ku ofesi ya nthambi pa galimoto ya Sosaite m’malo motumiza papositi.