Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Mwezi wa April, womwe tinachitanso Chikumbutso, tinagawira mabuku ndi timabuku 188,129. Tinagawiranso magazini okwana 492,454. Kuwonjezera pamenepa, tinachititsa maphunziro a Baibulo okwana 99,640 ndipo tinathera maola 1,384,091 mu utumiki wakumunda. M’mwezi umenewunso abale ndi alongo 8,033 anadzipereka kuchita upainiya wothandiza. Tikukuthokozani kwambiri abale chifukwa cha khama lanu pa nyengo ya Chikumbutso. Sitikukayikira kuti Yehova apitiriza kudalitsa khama lathu pamene tikumvera lamulo la Yesu loti tizilalikira ndi kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira ake.—Mat. 28:19-20.