Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Posachedwapa, m’bale wina anayamikira kwambiri ntchito yophunzitsa anthu Baibulo. Iye anati: “Ndakhala ndikugwira ntchito kwa zaka 26 ngati wapolisi. Ndinaphunzira zambiri zokhudza chitetezo koma tsopano ndikuona kuti ndinaphunzira zinthu zochepa kwambiri ndikayerekezera ndi zimene ndaphunzitsidwa ndi gulu la Yehova za chitetezo chenicheni.” Panopo munthu ameneyu anasiya ntchito ya polisi. Iye ndi m’bale wobatizidwa ndipo akugwira nawo ntchito yophunzitsa anthu Baibulo.