Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/12 tsamba 8
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
km 7/12 tsamba 8

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu July ndi August: Ofalitsa angagawire timabuku ta masamba 32 totsatirati: Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere, kapena kakuti, Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani? Ngati mukuona kuti munthu amene mwakumana naye amavutika kuwerenga, mungamugawire kabuku kakuti, Mverani Mulungu kapena Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. Popanga maulendo obwereza, sonyezani mwininyumba buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo. September ndi October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pochita maulendo obwereza, mungayambitse phunziro la Baibulo pogwiritsira ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ngati mukuona kuti n’koyenera mungamugawire timabuku takuti, Mverani Mulungu ndi Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo.

◼ CD ya nyimbo ya mutu wakuti, Sing to Jehovah—Vocal Renditions, Disc 5 ituluka posachedwapa ndipo mungakopere pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya jw.org kuyambira pa August 1. Poyamba nyimbo zimenezi zidzayamba kupezeka m’Chingelezi ndipo kenako zidzayamba kupezeka m’zinenero zinanso. Mungaitanitse ma CD a nyimbozi kudzera mu mpingo. Tikulimbikitsa onse amene ali ndi mwayi wogwiritsa ntchito Intaneti kuti akopere nyimbozi pa adiresi yathu m’malo moitanitsa ma CD. Tikutero chifukwa kukopera nyimbozi pa Intaneti ndi kotsikirapo mtengo poyerekeza ndi kuitanitsa ma CD. Dziwani kuti ma Disc 1 mpaka 4 anatulutsidwa kale.

◼ Mipingo yonse iyambe kuitanitsa Kalendala ndi timabuku ta Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku ta 2013 mwamsanga polemba ndi kutumiza Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Maoda onse ayenera kufika ku ofesi ya nthambi pasanafike pa October 15, 2012. Tibwerezenso kuti mipingo yonse ilembe ndi kutumiza ku ofesi ya nthambi oda ya zinthu zimenezi pasanafike pa October 15, 2012. Ngati simuchita zimenezi ndiye kuti abale ndi alongo sadzalandira zinthu zofunika kwambirizi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena