Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu August: Ofalitsa angagawire timabuku totsatirati: Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?, kapena kakuti, Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere. Popanga maulendo obwereza, sonyezani mwininyumba buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo. September ndi October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pochita maulendo obwereza, mungayambitse phunziro la Baibulo pogwiritsira ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. November: Ofalitsa angagawire timapepala totsatirati: Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa, Yehova—Kodi Iye Ndani?, Yesu Khristu—Kodi Iye Ndani?, kapena Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Ngati mwapeza anthu achidwi, asonyezeni mmene timaphunzirira Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena timabuku takuti Mverani Mulungu ndiponso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha.