Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Mwezi wa June chaka chino, tinathera maola 1,268,035 pa ntchito yophunzitsa anthu zokhudza Ufumu wa Mulungu. Zimenezi zikusonyeza kuti wofalitsa aliyense anathera maola pafupifupi 16 ali mu utumiki wakumunda. Tikukuyamikirani kwambiri abale ndi alongo chifukwa chogwira ntchito yolalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu’ mwakhama ngakhale kuti mukukumana ndi mavuto osiyanasiyana.—Mat. 24:14; 28:19, 20.