Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Nyumba ya Ufumu ya mpingo wa Milombwa m’dera la C-04 inamalizidwa kumangidwa pa February 16, 2012. Malipoti akusonyeza kuti pamene abale ndi alongo ankamanga Nyumba ya Ufumuyi, tsiku lililonse anthu pafupifupi 42, omwe si Mboni, ankabwera kudzaona mmene ntchitoyi inkayendera. Anthu ambiri anachita chidwi chifukwa cha kugwirizana ndiponso kugwira ntchito kwathu mwakhama. Pakali pano m’Malawi muno muli Nyumba za Ufumu zoposa 1,060. Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu wathu Yehova ndi wowolowa manja ndipo tikumuthokoza chifukwa chopereka malo abwino olambirira amenewa kwa anthu ake mopanda tsankho.—Mac. 10:34, 35.