Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu January ndi February 2013: Gawirani timabuku totsatirati: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu kapena Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Pochita maulendo obwereza, gwiritsani ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo ngati zili zoyenerera mogwirizana ndi mwininyumbayo, gwiritsani ntchito timabuku takuti, Mverani Mulungu ndiponso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha, ndipo yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo. March ndi April 2013: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati zili zoyenerera mogwirizana ndi mwininyumbayo, gwiritsani ntchito timabuku takuti, Mverani Mulungu ndiponso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. Pochita maulendo obwereza, gwiritsani ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo.
◼ Kuyambira mwezi wa February 2013, oyang’anira dera adzayamba kukamba nkhani ya onse ya mutu wakuti, “Uthenga Wabwino . . . Kudziko Lililonse, Fuko Lililonse, Chinenero Chilichonse.”