Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Pa Mateyu 21:16 timawerenga kuti: “M’kamwa mwa ana ndi mwa ana oyamwa mwaikamo mawu otamanda.” Mogwirizana ndi zimenezi, tsiku lina kamtsikana kena ka zaka zitatu, dzina lake Estere, kankalalikira ndi mayi ake kunyumba ndi nyumba. Kenako anaima penapake kuti apume. Estere ataona amayi ena akudutsa, anaganiza zowalalikira. Anawapatsa kapepala kakuti, Sangalalani ndi Moyo Wabanja. Estere anangouza mayiwo kuti: “Kapepalaka kakunena za banja.” Mayiyo anasangalala kwambiri ndi kapepalako chifukwa anali ndi mavuto a m’banja. Izi zikusonyeza kuti ndi bwinodi kuphunzitsa ana athu kutamanda Yehova.—Miy. 22:6.