Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu: August: Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu, Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani?, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. September ndi October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! November: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kapena mungagawire timapepala iti: Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?, Sangalalani ndi Moyo Wabanja, Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko? ndi Moyo m’Dziko Latsopano la Mtendere.
◼ Kuyambira mlungu woyambira September 16, 2013, tidzayamba kuphunzira buku lakuti Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya pa Phunziro la Baibulo la Mpingo. Mipingo imene ilibe mabuku okwanira iitanitse mabukuwa pamene ikuitanitsa mabuku ulendo wotsatira.
◼ Kufunsa Komanso Kuitanitsa Mabuku: Tsopano mukhoza kuitanitsa mabuku ndi maganizi kapena kufunsa zilizonse zokhudza mabuku amene mwalandira kapena kutidziwitsa za amene simunalandire pogwiritsa ntchito imelo adiresi iyi: shipping.mw@jw.org. Kumbukirani kuti ngati Nyumba ya Ufumu yanu imagwiritsidwa ntchito ndi mipingo ingapo, muyenera kuitanitsa zinthu pogwiritsa ntchito mpingo woimira za mabuku, kupatulapo ngati mukuitanitsa zinthu zoitanitsa mwapadera.