Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu: September: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! October: Ntchito yathu yaikulu idzakhala kugawira Uthenga wa Ufumu Na. 38. November: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kapena kabuku kamodzi mwa timapepala iti: Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?, Sangalalani ndi Moyo Wabanja, Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere, Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko? December: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
◼ Nkhani yapadera ya panyengo ya Chikumbutso cha 2014 idzakambidwa mlungu woyambira April 21. Mutu wa nkhaniyi udzalengezedwa m’tsogolo muno. Mipingo imene idzakhale ndi woyang’anira dera kapena msonkhano wadera mlungu umenewo idzakhale ndi nkhaniyi mlungu wotsatira. Mpingo uliwonse usadzakhale ndi nkhaniyi pasanafike pa April 21.