Zochitika mu Utumiki Wakumunda
M’mwezi wa May chaka chino, mlongo wina yemwe akutumikira pa Beteli ankapita kwawo kumpoto kwa dziko lino kukaona mayi ake. Pa ulendowu anatenga magazini okwana 60 oti azigawira anthu. Ali m’basi, anagawira magazini a Galamukani! awiri kwa Rasi amene anakhala naye pafupi. Kenako anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize kugawira magazini onse amene anali nawo. Atayenda kwa maola awiri, tayala la basiyo linaphulika ndipo aliyense anatsika. Panalibe tayala lina loti akanatha kuikirira choncho onse anadikirira tayala lina kuchokera ku Lilongwe. Zimenezi zinachititsa kuti akhale pamalowa kwa maola atatu. Mlongoyu anayamba kulalikira kwa anthu amene anakwera m’basiyo ndipo anayankha kuchokera m’Baibulo mafunso osiyanasiyana amene anthuwo ankamufunsa. Ambiri anachita chidwi kuti mlongoyu anayenda ndi Baibulo pa ulendowu. Analalikiranso munthu wina wa ku Australia amene anali asanalalikiridwepo ndi Mboni za Yehova. Pa ulendowu komanso pobwerera, mlongoyu anagawira magazini 50 ndi timabuku tiwiri. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tiyenera kumakhala okonzeka kuyankha aliyense amene watifunsa za chiyembekezo chathu.—1 Pet. 3:15.