Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu February: Kabuku ka masamba 32 kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu, Mverani Mulungu kapena kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. March ndi April: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! May ndi June: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kapena timapepala totsatirati: Kodi Baibulo Mumalikhulupirira? Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo? Kodi N’chiyani Chingathandize Kuti Banja Likhale Losangalala? Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani? ndi kakuti Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?
◼ Nkhani yapadera ya onse ya panyengo ya Chikumbutso cha 2014 idzakhala ya mutu wakuti, “N’chifukwa Chiyani Mulungu Yemwe ndi Wachikondi Amalola Kuti Tizivutika?”