Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Kwa nthawi yoyamba m’Malawi, mabanja 10 ochokera m’dziko lathu lino komanso mabanja awiri ochokera ku Mozambique anachita mwambo womaliza maphunziro awo. Anachita mwambowu ataphunzira kwa miyezi iwiri m’kalasi yoyamba ya Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja imene inachitika m’Chichewa. Mwambowu unachitika Lamlungu pa October 27, 2013. N’zosakayikitsa kuti mabanja amenewa akathandiza mipingo imene atumizidwako. Tikukhulupiriranso kuti mabanja ambiri akonza zoti adzalowe sukuluyi m’tsogolomu.