Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu September ndi October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! November ndi December: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kapena kapepala kakuti, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?
◼ Nkhani yapadera ya panyengo ya Chikumbutso cha 2015 idzakambidwa pa mlungu woyambira April 6. Mutu wa nkhaniyi tidzakudziwitsanibe. Mipingo imene idzakhale ndi mlungu wapadera kapena msonkhano pa mlungu umenewu, idzakambe nkhaniyi mlungu wotsatira. Dziwani kuti nkhaniyi siyenera kukambidwa mlungu wa April 6 usanafike.
◼ Kuyambira mwezi wa September, oyang’anira dera azidzakamba nkhani ya mutu wakuti, “Kodi Nzeru Yochokera kwa Mulungu Ingatithandize Bwanji?”