Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Yehova akudalitsa kwambiri ntchito yathu yolalikira m’Malawi muno. Mwachitsanzo, chaka cha utumiki cha 2014 chomwe changothachi, mipingo yatsopano yokwana 35 inakhazikitsidwa. Sitikukayikira kuti Yehova apitiriza kudalitsa utumiki wathu m’chaka cha utumiki cha 2015.—Mal. 3:10.