Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu August: Timabuku takuti, Mverani Mulungu, Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha ndi Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu. September ndi October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! November: Buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kapena timapepala tatsopano totsatirati: Kodi Baibulo Mumalikhulupirira?, Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani?, Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?, Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?, Kodi N’chiyani Chingathandize Kuti Banja Likhale Losangalala?, Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka? ndi kakuti, Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
◼ Kuyambira mu September, woyang’anira dera azidzakamba nkhani ya onse ya mutu wakuti, “Kodi Malangizo a Mulungu Ndi Othandizadi?”
◼ Makalasi Ophunzitsa Kuwerenga ndi Kulemba: Ngati sukuluyi sikuchitika mumpingo mwanu, konzani zoti iyambe n’cholinga choti muthandize abale ndi alongo omwe sadziwa kulemba ndi kuwerenga. Izi zingawathandize kuti azitha kuwerenga okha Baibulo komanso mabuku athu. Zingawathandizenso kuti aziphunzitsa ana awo mogwira mtima.