July 17-23
EZEKIELI 18-20
Nyimbo Na. 21 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kodi Yehova Akatikhululukira Machimo, Amawakumbukirabe?”: (10 min.)
Ezek. 18:19, 20—Yehova amaimba mlandu munthu aliyense malinga ndi zochita zake (w12 7/1 18 ¶2)
Ezek. 18:21, 22—Yehova ndi wokonzeka kukhululukira anthu amene alapa ndipo akatero samawaimbanso mlandu (w12 7/1 18 ¶3-7)
Ezek. 18:23, 32—Yehova amawononga oipa pokhapokha ngati wawachenjeza koma sakufuna kusintha (w08 4/1 8 ¶4; w06 12/1 27 ¶11)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Ezek. 18:29—N’chifukwa chiyani Aisiraeli anayamba kuganiza kuti Yehova akulakwitsa zinthu, nanga kodi ifeyo tingapewe bwanji mtima umenewu? (w13 8/15 11 ¶9)
Ezek. 20:49—Kodi n’chifukwa chiyani anthu ankaganiza kuti Ezekieli ‘akunena miyambi,’ nanga ifeyo tikupezapo chenjezo lotani? (w07 7/1 14 ¶3)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Ezek. 20:1-12
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) 1 Yoh. 5:19—Kuphunzitsa Choonadi. Muuzeni nkhani imene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Gen. 3:2-5—Kuphunzitsa Choonadi. Muuzeni nkhani imene mudzakambirane ulendo wotsatira. (Onani mwb16.08 8 ¶2.)
Nkhani: (Osapitirira 6 min.) w16.05 32—Mutu: Kodi Tingasonyeze Bwanji Kusangalala Tikamva Chilengezo Choti Munthu Wina Wabwezeretsedwa?
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Kodi Mumadziimbabe Mlandu Yehova Akakukhululukirani?”: (10 min.) Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuonetsa vidiyo yakuti Muzitsatira Mokhulupirika Mfundo za Yehova—Muzikhululuka.
Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake?: (5 min.) Kambiranani nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake?” Yambani ndi kumvetsera nkhaniyi pa gawo lakuti “Kodi Inuyo Mungatani?”
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 4 ¶1-6, komanso tsamba 43
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 38 ndi Pemphero