October 30–November 5
YOWELI 1-3
Nyimbo Na. 143 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Ana Anu Aamuna ndi Ana Anu Aakazi Adzanenera”: (10 min.)
[Onetsani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yoweli.]
Yow. 2:28, 29—Akhristu odzozedwa amagwira ntchito monga aneneri a Yehova (w02 8/1 15 ¶4-5; jd 167 ¶4)
Yow 2:30-32—Okhawo amene amaitanira pa dzina la Yehova ndi amene adzapulumuke pa tsiku lake la chiweruzo (w07 10/1 13 ¶2)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Yow. 2:12, 13—Kodi mavesi amenewa akutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya kulapa mochokera pansi pa mtima? (w07 10/1 13 ¶5)
Yow 3:14—Kodi ‘chigwa choweruzira mlandu’ n’chiyani? (w07 10/1 13 ¶3)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yow. 2:28–3:8
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Khadi lodziwitsa anthu za JW.ORG.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Khadi lodziwitsa anthu za JW.ORG., limene munagawira pa ulendo woyamba. Pomaliza mufotokozereni za vidiyo iliyonse ya pa jw.org.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) lv 197 ¶3-5
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Yehova Amatithandiza Kuti Tipirire Mayesero: (9 min.) Onetsani vidiyo yakuti Yehova Ndi Nsanja Yanga Yolimba. Kenako funsani omvetsera mafunso awa: Kodi banja la a Henschel linakumana ndi mayesero otani? Kodi kukhulupirika kwa makolo kumathandiza bwanji ana? Kodi Yehova angakulimbikitseni bwanji ngati mmene anachitira ndi M’bale Henschel?
Khalani Bwenzi la Yehova—Dzina la Yehova: (6 min.) Onetsani vidiyo yakuti Khalani Bwenzi la Yehova—Dzina la Yehova. Kenako pemphani ana amene munawasankhiratu kuti abwere kupulatifomu ndipo muwafunse mafunso otsatirawa: Kodi dzina la Yehova limatanthauza chiyani? Kodi Yehova analenga zinthu ziti? Kodi Yehova angakuthandize bwanji iweyo?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 9 ¶10-15, komanso tsamba 90, 93, 96-97
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 72 ndi Pemphero