August 20-26
Luka 21-22
Nyimbo Na. 27 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Chipulumutso Chanu Chikuyandikira”: (10 min.)
Luka 21:25—Pa chisautso chachikulu padzachitika zinthu zochititsa mantha (kr 226 ¶9)
Luka 21:26—Adani a Yehova adzasowa chochita
Luka 21:27, 28—Yesu akadzabwera adzapulumutsa anthu okhulupirika (w16.01 10-11 ¶17; w15 7/15 17 ¶13)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Luka 21:33—Kodi mawu a Yesu palembali akutanthauza chiyani? (“Kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka” “mawu anga sadzachoka ayi” mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 21:33, nwtsty)
Luka 22:28-30—Kodi ndi pangano liti limene Yesu anakhazikitsa ndipo anapangana ndi ndani, nanga lidzakwaniritsa chiyani? (w14 10/15 16-17 ¶15-16)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Luka 22:35-53
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Yambani ndi chitsanzo cha zimene tinganene. Kenako sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri.
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha zimene tinganene. Kenako sonyezani zimene mungachite ngati mwininyumba ali wotanganidwa.
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zofunika Pampingo: (15 min.)
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 1
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 96 ndi Pemphero