Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb18 August tsamba 7
  • Yesu Anaferanso M’bale Wakoyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anaferanso M’bale Wakoyo
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Nkhani Yofanana
  • Pitirizani Kuchita Zinthu Mogwirizana Mumpingo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Khalani ndi Maganizo a Khristu
    Nsanja ya Olonda—2009
  • “Mukhale Nacho Chikondano Chenicheni mwa Inu Nokha”
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Musamakhumudwitse “Tianati”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18 August tsamba 7
Yesu akulankhula ndi otsatira ake

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Yesu Anaferanso M’bale Wakoyo

Yesu anapereka moyo wake nsembe chifukwa cha anthu ochimwa. (Aroma 5:8) Sitikukayikira kuti mumayamikira chikondi chimene Yesu anatisonyezachi. Komabe nthawi zina timafunika kuchita kudzikumbutsa kuti Yesu anaferanso abale athu. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda abale ndi alongo athu, omwe nawonso ndi ochimwa ngati ife tomwe? Tingachite zimenezi m’njira zitatu zotsatirazi. Choyamba, m’malo momangocheza ndi anthu okhawo amene tinazolowerana nawo, tingachite bwino kumachezanso ndi anthu amene timasiyana nawo m’zinthu zambiri. (Aroma 15:7; 2 Akor. 6:12, 13) Chachiwiri, tiyenera kupewa kuchita kapena kulankhula zinthu zomwe zingakhumudwitse ena. (Aroma 14:13-15) Ndipo chomaliza, wina akatilakwira tiyenera kumakhululuka mwansanga. (Luka 17:3, 4; 23:34) Ngati titamayesetsa kutsanzira Yesu pochita zinthu zimenezi, Yehova angadalitse mpingo wathu ndi mtendere komanso mgwirizano.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, MUZIONA ZINTHU MOYENERA NDIPO KENAKO KAMBIRANANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Miki walandiridwa bwino mumpingo wake watsopano

    Kodi Miki ankaona bwanji anthu a mumpingo wake atangosamukiramo kumene?

  • Miki sakusangalala ndi anthu ena mumpingo

    Kodi n’chiyani chimene chinachititsa kuti asinthe mmene ankawaonera?

  • Yesu akukomera mtima atumwi ake ngakhale wawapeza akugona

    Kodi chitsanzo cha Yesu chinamuthandiza bwanji pa nkhaniyi? (Maliko 14:38)

  • Miki akuseka kamnyamata komwe kamathamanga katamugunda ndipo juwisi yemwe amamwa watayikira pazovala zake

    Kodi lemba la Miyambo 19:11 lingatithandize bwanji kuti tiziona Akhristu anzathu moyenera?

FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA:

Kodi ndi zinthu ziti zomwe anthu ena anandilakwira zomwe ndingangozinyalanyaza?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena