MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Yehova Anatithandiza Kulera Ana Athu
Kodi makolo angaphunzire chiyani kuchokera kwa Atate wathu Yehova, zomwe zingawathandize kuti alere bwino ana awo? Onerani vidiyo yakuti Yehova Anatithandiza Kulera Ana Athu, yonena za banja la a Abilio ndi a Ulla Amorim ndipo kenako yankhani mafunso otsatirawa:
Kodi kuganizira mmene makolo awo anawalerera kunathandiza bwanji a Abilio ndi a Ulla kuti alere bwino ana awo?
Kodi ana awo amakumbukira zinthu zosangalatsa ziti zimene zinkachitika ali aang’ono?
Kodi a Abilio ndi a Ulla anagwiritsa ntchito bwanji mfundo za pa Deuteronomo 6:6, 7?
N’chifukwa chiyani iwo sankangouza ana awo malamulo oti azitsatira?
Kodi anathandiza bwanji ana awo kuti paokha akonze tsogolo lawo?
Ndi zinthu ziti zimene anadzimana chifukwa cholimbikitsa ana awo kuchita utumiki wa nthawi zonse? (bt 178 ¶19)