July 8-14
1 ATESALONIKA 1-5
Nyimbo Na. 90 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Pitirizani Kutonthozana ndi Kulimbikitsana”: (10 min.)
[Onerani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 1 Atesalonika.]
1 Ates. 5:11-13—Muzipereka “ulemu waukulu” kwa amene akutsogolera pakati panu (w11 6/15 26 ¶12; 28 ¶19)
1 Ates. 5:14—Muzilimbikitsa anthu amene ali ndi nkhawa komanso muzithandiza ofooka (w17.10 10 ¶13; w15 2/15 9 ¶16)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
1 Ates. 4:3-6—Kodi munthu amene wachita dama ‘amapweteka m’bale wake komanso kumuphwanyira ufulu’ m’njira yotani? (it-1 863-864)
1 Ates. 4:15-17—Kodi ndi ndani amene ‘adzatengedwe m’mitambo n’kukakumana ndi Ambuye m’mlengalenga,’ nanga zimenezi zidzachitika bwanji? (w15 7/15 18-19 ¶14-15)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) 1 Ates. 3:1-13 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. (th phunziro 1)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri. (th phunziro 3)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri. (th phunziro 4)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Apainiya Amatilimbikitsa Kwambiri: (9 min.) Onerani vidiyo yakuti, Apainiya Muli ndi Udindo Wothandiza Ena. (pitani pa mavidiyo a BAIBULO). Kenako yankhani mafunso otsatirawa: Kodi apainiya angalimbikitse bwanji ena mumpingo? Kodi apainiya a mumpingo wanu anakulimbikitsani bwanji?
Timalimbikitsidwa ndi Anthu Achitsanzo Chabwino: (6 min.) Onerani vidiyo yakuti, Tiyenera ‘Kuthamanga Mopirira’—Muzitsanzira Anthu Achitsanzo Chabwino. Kenako yankhani mafunso otsatirawa: Kodi mlongoyu anali ndi vuto lotani? Kodi anatani kuti anthu ena amulimbikitse?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 43 ndime 1-7
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 68 ndi Pemphero