CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 6-8
“Anachitadi Momwemo”
Taganizirani ntchito imene Nowa ndi banja lake anali nayo kuti amange chingalawa popanda zipangizo komanso njira zamakono zomangira.
Chingalawacho chinali chachikulu kwambiri. Chinali cha mamita 133 m’litali, mamita 22 m’lifupi komanso mamita 13 kupita m’mwamba
Ankafunika kugwetsa mitengo, kuidula, kenako n’kuipititsa kumene ankagwirira ntchito
Ankafunika kupaka phula mkati komanso kunja kwa chingalawacho
Ankafunikanso kusunga chakudya cha chaka chathunthu cha iyeyo ndi banja lake komanso zinyama
Ntchitoyi iyenera kuti inatenga zaka 40 kapena 50 kuti ithe
Kodi nkhaniyi ingatithandize bwanji ngati timaona kuti n’zovuta kuchita zimene Yehova amatiuza?