CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 42-43
Yosefe Anasonyeza Kudziletsa Kwambiri
Kodi mukuganiza kuti Yosefe anamva bwanji atakumana ndi azichimwene ake mosayembekezereka? Iye akanatha kudzidziwikitsa kwa azichimwene akewo nthawi yomweyo kenako n’kuwakumbatira, kapena akanatha kuwabwezera zachipongwe zomwe anamuchitira. Koma sanachite zinthu mopupuluma. Ndiye kodi inuyo mungatani ngati anthu a m’banja lanu kapena anthu ena atakuchitirani zinthu zopanda chilungamo? Chitsanzo cha Yosefe chikutiphunzitsa kufunika kokhala odziletsa komanso kuchita zinthu modekha m’malo motsatira mtima wathu wonyenga n’kumachita zinthu mopupuluma.
Kodi mungatsanzire bwanji Yosefe pa mavuto amene mumakumana nawo?