July 6-12
EKISODO 6-7
Nyimbo Na. 150 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Tsopano Uona Zimene Ndichite kwa Farao”: (10 min.)
Eks 6:1—Mose ankayembekezera kuona “dzanja lamphamvu” la Yehova
Eks 6:6, 7—Yehova anauza Aisiraeli kuti adzawalanditsa (it-2 436 ¶3)
Eks 7:4, 5—Yehova ananena kuti Farao ndi Aiguputo adzadziwa kuti iye ndi Mulungu woona (it-2 436 ¶1-2)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Eks 6:3—Kodi Yehova ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti sanadzidziwikitse kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo? (it-1 78 ¶3-4)
Eks 7:1—Kodi Mose anakhala bwanji “Mulungu” kwa Farao, nanga Aroni anakhala bwanji “mneneri” wake? (it-2 435 ¶5)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Eks 6:1-15 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti, Kuwafika Pamtima Anthu, kenako kambiranani phunziro 19 m’kabuku ka Kuphunzitsa.
Nkhani: (Osapitirira 5 min.) w15 1/15 9 ¶6-7—Mutu: Muziyamikira Yehova Tsiku Lililonse. (th phunziro 19)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zofunika Pampingo: (15 min.)
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 90
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 147 ndi Pemphero