July 13-19
EKISODO 8-9
Nyimbo Na. 12 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Farao Yemwe Anali Wonyada Anathandiza Kukwaniritsa Cholinga cha Mulungu Mosadziwa”: (10 min.)
Eks 8:15—Farao anaumitsa mtima wake ndipo sanamvere Mose ndi Aroni (it-2 1040-1041)
Eks 8:18, 19—Farao anaumitsabe mtima wake ngakhale kuti ochita zamatsenga ake anavomereza kuti sangathe kuchita zimene Yehova anachita
Eks 9:15-17—Mwa kulola Farao kukhalabe ndi moyo, Yehova anachititsa kuti dzina lake lilemekezedwe (it-2 1181 ¶3-5)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Eks 8:21—Kodi tizilombo totchulidwa palembali tinali toopsa bwanji? (it-1 878)
Eks 8:25-27—N’chifukwa chiyani Mose ananena kuti nsembe za Aisiraeli zikanakhala “chonyansa cha Aiguputo”? (w04 3/15 25 ¶9)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Eks 8:1-19 (th phunziro 12)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi, ndipo kenako funsani mafunso otsatirawa: Kodi wofalitsayu anatani mwininyumba atasonyeza kuti sakufuna kukambirana naye? Kodi wofalitsayu akanatani kuti agawire buku kapena kabuku kopezeka pa Zinthu Zophunzitsira?
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. (th phunziro 6)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 3)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako m’patseni buku kapena kabuku kamene timagwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu. (th phunziro 12)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muzidzichepetsa—Muzipewa Kudzitama”: (7 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Khalani Bwenzi la Yehova—Uzidzichepetsa. Kenako itanani ana omwe munawasankhiratu kuti abwere kutsogolo ndipo muwafunse mafunso okhudza vidiyoyi.
“Muzidzichepetsa Ena Akamakuyamikirani”: (8 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Muzikhala Okhulupirika Ngati Mmene Yesu Analili—Pamene Anthu Ena Akukuyamikirani.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 91
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 151 ndi Pemphero