SEPTEMBER 7-13
EKISODO 23-24
Nyimbo Na. 34 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Musamatsatire Khamu la Anthu”: (10 min.)
Eks 23:1—Musamafalitse nkhani zabodza zimene mwamva (w18.08 4 ¶7-8)
Eks 23:2—Musamatengeke ndi anthu kuti muchite zoipa (it-1 11 ¶3)
Eks 23:3—Musamakondere (it-1 343 ¶5)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Eks 23:9—Kodi Yehova anawauza chiyani Aisiraeli pofuna kuwathandiza kuti azisonyeza chifundo? (w16.10 9 ¶4)
Eks 23:20, 21—Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti mngelo wotchulidwa mulembali ndi Mikayeli? (it-2 393)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Eks 23:1-19 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi ndipo kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Mwininyumba atayankha molakwika, kodi wofalitsa ananena zotani kuti apitirize kukambirana naye? Kodi wofalitsayu akananenanso zotani kuti agawire Nsanja ya Olonda yogawira Na. 3 2020?
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako musonyezeni ndi kukambirana naye mfundo za m’vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? (koma musaonetse vidiyoyi). (th phunziro 1)
Nkhani: (Osapitirira 5 min.) w16.05 30-31—Mutu: Kodi Mkhristu Angadziwe Bwanji Ngati N’zoyenera Kupereka Ndalama kwa Ogwira Ntchito M’boma? (th phunziro 14)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Musamafalitse Nkhani Zabodza”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yamakatuni yakuti Kodi Ndingatani Kuti Ndithetse Miseche?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (Osapitirira 30 min.) jy mutu 99
Mawu Omaliza (Osapitirira 3 min.)
Nyimbo Na. 85 ndi Pemphero