MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Njira Zitatu Zimene Zingatithandize Kuti Tizidalira Yehova
Davide anagonjetsa Goliyati chifukwa ankadalira Yehova. (1Sa 17:45) Yehova amafuna kusonyeza mphamvu zake kwa atumiki ake. (2Mb 16:9) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timadalira nzeru za Yehova m’malo momadalira mphamvu kapena nzeru zathu? Onani njira zitatu zotsatirazi:
Tizipemphera nthawi zonse. Tisamangopemphera kuti Yehova atikhululukire tikalakwitsa chinachake koma kutinso atipatse mphamvu kuti tikwanitse kulimbana ndi mayesero. (Mt 6:12, 13) Tisamangopemphera kuti Yehova adalitse zomwe tasankha koma tizipempha kuti atitsogolere komanso atipatse nzeru tisanasankhe zochita.—Yak 1:5
Tizikhala ndi ndandanda yowerengera komanso kuphunzira Baibulo. Tiziwerenga Baibulo tsiku lililonse. (Sl 1:2) Tiziganizira kwambiri zitsanzo za m’Baibulo komanso tizigwiritsa ntchito zimene tikuphunzirapo. (Yak 1:23-25) Tizikonzekera tikamapita mu utumiki m’malo momangodalira luso limene tili nalo. Tizikonzekera misonkhano kukadali nthawi n’cholinga choti tikapindule mokwanira
Tizichita zinthu mogwirizana ndi gulu la Yehova. Tizidziwa mfundo zatsopano zimene gulu likuyendera ndipo tizitsatira mwamsanga zinthu zikasintha. (Nu 9:17) Tizimvera akulu akamatipatsa malangizo komanso uphungu.—Ahe 13:17
ONERANI VIDIYO YAKUTI PALIBE CHIFUKWA CHOTI TIZIOPA KUZUNZIDWA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
• Kodi abale ndi alongo ankaopa chiyani?
• Kodi n’chiyani chinawathandiza kuti athetse manthawa?