July 18-24
2 SAMUELI 22
Nyimbo Na. 4 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Muzidalira Yehova Kuti Akuthandizeni”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
2Sa 22:36—Kodi kudzichepetsa kwa Yehova kunakweza bwanji Davide? (w12 11/15 17 ¶7)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) 2Sa 22:33-51 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (3 min.) Yambani ndi nkhani imene ili mu chitsanzo cha ulendo woyamba. Mugawireni chimodzi mwa Zinthu Zophunzitsira. (th phunziro 1)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi nkhani imene ili mu chitsanzo cha ulendo wobwereza. Kenako mugawireni kabuku kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale ndipo yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? (th phunziro 3)
Nkhani: (5 min.) w06 8/15 21 ¶7-8—Mutu: Kodi Satana Ndi Amene Amachititsa Vuto Lililonse Lomwe Timakumana Nalo? (th phunziro 13)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Tizisangalala Ndi Zimene Yehova Amachita Populumutsa Anthu Ake: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako funsani mafunso awa: Kodi Yehova anathandiza bwanji M’bale Ganeshalingam ndi anthu a m’banja lake panthawi imene ku Sri Lanka kunali nkhondo yapachiweniweni? Kodi zimenezi zalimbitsa bwanji chikhulupiriro chanu?
Zofunika Pampingo: (10 min.)
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lff kubwereza gawo 1
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 60 ndi Pemphero