Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb22 July tsamba 15
  • Kodi Mumayesetsa Kuona Mmene Yehova Akuyankhira Mapemphero Anu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumayesetsa Kuona Mmene Yehova Akuyankhira Mapemphero Anu?
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Nkhani Yofanana
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Mmene Yehova Amayankhira Mapemphero Athu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kodi Ndimapemphero Ayani Omwe Amayankhidwa?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Yehova Amayankha Mapemphero Anga?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwb22 July tsamba 15
Mlongo akupemphera. Baibulo lake lili patebulo.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mumayesetsa Kuona Mmene Yehova Akuyankhira Mapemphero Anu?

M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za mapemphero amene Mulungu anayankha. Atumiki a Mulungu ataona mmene iye anayankhira mapemphero awo komanso mmene anawathandizira, chikhulupiriro chawo chinalimba kwambiri. Choncho nafenso tiyenera kumapereka mapemphero achindunji kenako n’kumaona mmene Yehova akutiyankhira. Koma tizikumbukira kuti nthawi zina akhoza kutiyankha zosiyana ndi zimene tinapempha kapenanso zoposa zimene tinapempha. (2Ak 12:7-9; Aef 3:20) Kodi Yehova angatiyankhe m’njira ziti?

  • Angatithandize kukhala ndi mphamvu, kukhazikitsa mtima m’malo kapena kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kuti tithe kulimbana ndi mavuto.​—Afi 4:13

  • Angatipatse nzeru kuti tizisankha zinthu moyenera.​—Yak 1:5

  • Angatithandize kuchita zimene iye amakonda.​—Afi 2:13

  • Angatithandize kudekha tikapanikizika ndi nkhawa.—Afi 4:6, 7

  • Angatithandize pogwiritsa ntchito anthu ena.—1Yo 3:17, 18

  • Angathandize anthu amene timawapempherera.—Mac 12:5, 11

ONERANI VIDIYO YAKUTI YEHOVA NDI “WAKUMVA PEMPHERO,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi zimene M’bale Shimizu anakumana nazo zingatilimbikitse bwanji ngati tikulephera kuchita zinthu zina chifukwa cha mavuto a thanzi?

  • Kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo cha M’bale Shimizu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena