MARCH 4-10
MASALIMO 16-17
Nyimbo Na. 111 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. ‘Zinthu Zonse Zabwino Zimachokera kwa Yehova’
(10 min.)
Kukhala pa ubwenzi ndi anthu amene amatumikira Yehova kumatithandiza kukhala osangalala (Sl 16:2, 3; w18.12 26 ¶11)
Kudziwa kuti Yehova ndi mnzathu kumatithandiza kukhala osangalala kwambiri (Sl 16:5, 6; w14 2/15 29 ¶4)
Timamva kuti Yehova ali nafe chifukwa amatiteteza mwauzimu (Sl 16:8, 9; w08 2/15 3 ¶2-3)
Mofanana ndi Davide, timakhala ndi moyo wabwino kwambiri chifukwa chakuti nthawi zonse timachita zinthu zokhudza kulambira Yehova, yemwe amatipatsa zinthu zonse zabwino.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi panopa moyo wanga ukusiyana ndi mmene unalili ndisanaphunzire choonadi?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 17:1-15 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(1 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mugawireni kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso. (th phunziro 11)
5. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mugawireni kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso. Pambuyo poti munthuyo wasonyeza chidwi, yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti Tizikumbukira Imfa ya Yesu, kenako kambiranani naye mfundo za muvidiyoyi. (th phunziro 9)
6. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Mugawireni kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso. (th phunziro 2)
7. Kuphunzitsa Anthu
Nyimbo Na. 20
8. Kodi Tingakonzekere Bwanji Chikumbutso?
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Pomvera lamulo la Yesu, Lamlungu pa 24 March, tidzakumbukira imfa yake, yomwe imaphatikizapo chikondi chapadera chimene Yehova ndi Yesuyo anatisonyeza. (Lu 22:19; Yoh 3:16; 15:13) Kodi tingakonzekere bwanji mwambo wapaderawu?
Mugwire ndi mtima wonse ntchito yoitanira anthu kuti adzamvetsere nkhani yapadera komanso adzapezeke pa Chikumbutso. Mukonze ndandanda ya anzanu amene mungawaitanire. Ngati ena mwa anzanuwo sakhala m’gawo la mpingo wanu, mungaone pa jw.org kuti mupeze nthawi ndi malo amene mwambowu ukachitikire m’dera limene amakhala
Mungawonjezere zochita mu utumiki m’mwezi wa March ndi April. Kodi mungachite upainiya wothandiza wa maola 15 kapena 30?
Pa 18 March, mudzayambe kuwerenga zinthu zikuluzikulu zomwe zinachitika pa wiki yomaliza ya moyo wa Yesu ali padzikoli. Mungasankhe kuchuluka kwa zomwe mungawerenge tsiku lililonse kuchokera pa “Ndandanda Yowerengera Baibulo pa Nyengo ya Chikumbutso cha 2024” yomwe ili patsamba 6-7
Pa tsiku la Chikumbutso, mudzaonere pulogalamu yapadera ya Kulambira kwa M’mawa pa jw.org
Pa Chikumbutso, mudzalandire mwansangala alendo komanso ofalitsa amene anasiya kusonkhana. Mudzakhale okonzeka kuyankha mafunso omwe anthuwa angakufunseni pambuyo pa mwambowu. Mudzakonze zoti mudzayendere anthu omwe adzabwere pa mwambowu kuti mukawathandize kuphunzira zambiri
Mwambo wa Chikumbutso usanachitike komanso ukadzatha, muzidzaganizira za dipo
Onerani VIDIYO yakuti Tizikumbukira Imfa ya Yesu. Kenako funsani funso lotsatirali:
Kodi tingagwiritse ntchito bwanji vidiyoyi pamene tikuitanira anthu ku Chikumbutso?
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 6 ¶18-24, bokosi patsamba 48