Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 November tsamba 14-16
  • December 30, 2024–January 5, 2025

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • December 30, 2024–January 5, 2025
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 November tsamba 14-16

DECEMBER 30, 2024–JANUARY 5, 2025

MASALIMO 120-126

Nyimbo Na. 144 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Aisiraeli akukolola tirigu mosangalala.

Aisiraeli amene anabwerera kwawo akukolola mosangalala chifukwa choti Yehova wawadalitsa pa ntchito imene anagwira mwakhama

1. Anafesa Mbewu Akukhetsa Misozi, N’kukolola Akusangalala

(10 min.)

Aisiraeli anasangalala kwambiri pamene anamasulidwa ku ukapolo ku Babulo kuti akabwezeretse kulambira koona (Sl 126:1-3)

Amene anabwerera ku Yudeya n’kutheka kuti analira chifukwa cha ntchito yowawa imene ankafunika kugwira (Sl 126:5; w04 6/1 16 ¶10)

Koma anthuwo sanasiye ndipo analandira madalitso (Sl 126:6; w21.11 24 ¶17; w01 7/15 18-19 ¶13-14; onani chithunzi)

Aisiraeli akulima mwakhama. Wina akufesa mbewu pomwe wina akulima ndi pulawo.

FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Pambuyo poti tapulumutsidwa ku dziko loipali pa Aramagedo, kodi ndi zovuta ziti zomwe tingadzakumane nazo pogwira ntchito yaikulu yokonzanso dzikoli? Nanga tidzalandira madalitso otani?

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 124:2-5—Kodi tingayembekezere kuti Yehova azititeteza ngati mmene ankachitira ndi mtundu wa Aisiraeli? (cl 73 ¶15)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 124:1–126:6 (th phunziro 5)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. (lmd phunziro 3 mfundo 5)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pa ulendo wapita, munthuyo anasonyeza kuti sakhulupirira Baibulo. (lmd phunziro 9 mfundo 5)

6. Kuphunzitsa Anthu

(5 min.) lff phunziro 16 mawu oyamba ndi mfundo 1-3 (lmd phunziro 11 mfundo 3)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 155

7. Tizisangalala ndi Malonjezo a Mulungu

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Yehova anakwaniritsa zimene analonjeza anthu ake omwe anali ku ukapolo ku Babulo. Iye anawalanditsa komanso kuwachiritsa mwauzimu. (Yes 33:24) N’zoonekeratu kuti anawateteza limodzi ndi ziweto zawo kuti asagwidwe ndi mikango komanso zilombo zina zolusa zomwe zinachuluka m’dziko lawo pa nthawi imene simunkakhala anthu. (Yes 65:25) Iwo ankasangalala kukhala m’nyumba zawozawo komanso kudya zipatso za m’minda yawo ya mpesa. (Yes 65:21) Mulungu anadalitsa ntchito yawo ndipo anakhala ndi moyo wautali.—Yes 65:22, 23.

Zithunzi za muvidiyo yakuti “Tizisangalala ndi Malonjezo a Mulungu Okhudza Mtendere​—⁠Kachigawo Kake.” 1. Abale ndi alongo akucheza mosangalala. 2. Chithunzi cham’mwamba cha mapiri ndi nkhalango. 3. Mneneri Danieli amene waukitsidwa akuyenda m’nkhalango. 4. Banja likuhaga mwana wawo amene waukitsidwa. 5. Mbale ya zipatso ndi masamba. 6. Mathithi.

Waterfall: Maridav/stock.adobe.com; mountains: AndreyArmyagov/stock.adobe.com

Onerani VIDIYO yakuti Tizisangalala ndi Malonjezo a Mulungu Okhudza Mtendere—Kachigawo Kake. Kenako funsani mafunso otsatirawa:

  • Kodi maulosiwa akukwaniritsidwa bwanji masiku athu ano?

  • Kodi adzakwaniritsidwanso bwanji m’dziko latsopano?

  • Kodi ndi malonjezo ati amene mukuyembekezera kwambiri?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 20 ¶8-12, bokosi patsamba 161

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 58 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena