JULY 21-27
MIYAMBO 23
Nyimbo Na. 97 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Mfundo Zothandiza pa Nkhani ya Mowa
(10 min.)
Ngati mwasankha kuti muzimwa mowa, musamamwe wambiri (Miy 23:20, 21; w04 12/1 19 ¶5-6)
Muzikumbukira kuipa koledzera (Miy 23:29, 30, 33-35; it-1 656)
Musamapusitsike ndi maganizo akuti mowa si woipa (Miy 23:31, 32)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 23:21—Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kususuka ndi kunenepa? (w04 11/1 31 ¶2)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 23:1-24 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. (lmd phunziro 3 mfundo 5)
5. Ulendo Wobwereza
(5 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti mumuonetse mmene phunziro la Baibulo limachitikira. (lmd phunziro 9 mfundo 5)
6. Kuphunzitsa Anthu
(5 min.) Limbikitsani wophunzira wanu amene akulimbana ndi chizolowezi chimene Baibulo limaletsa. (lmd phunziro 12 mfundo 4)
Nyimbo Na. 35
7. Kodi Padzakhale Mowa Kapena Ayi?
(8 min.) Nkhani yokambirana.
Kodi anthu amene akukonza zochitika zinazake, mwachitsanzo phwando la ukwati, akuyenera kukonza zoti padzakhale mowa? Chimenechi ndi chosankha cha aliyense payekha. Koma munthu asanasankhe zoyenera kuchita pa nkhani imeneyi, akuyenera kuganizira mofatsa mfundo zingapo za m’Baibulo komanso zinthu zina.
Onerani VIDIYO yakuti Kodi Padzakhale Mowa Kapena Ayi? Kenako funsani mafunso awa:
Kodi mfundo za m’Baibulo zotsatirazi zingathandize bwanji anthu amene akukonza phwando kuganizira ngati pakuyenera kukakhala mowa kapena ayi?
Yoh 2:9—Yesu anasandutsa madzi kukhala vinyo pa phwando la ukwati.
1Ak 6:10—‘Zidakwa sizidzalowa mu Ufumu wa Mulungu.’
1Ak 10:31, 32—“Kaya mukudya kapena kumwa . . . , muzichita zinthu zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu. Muzipewa kukhumudwitsa.”
Kodi ndi zinthu zina ziti zimene mukuyenera kuziganizira?
Kuti tizisankha zinthu mwanzeru, n’chifukwa chiyani timafunika kugwiritsa ntchito “luso la kuganiza” n’cholinga choti tikwanitse kusankha mfundo za m’Baibulo zimene tingagwiritse ntchito?—Aro 12:1; Mla 7:16-18
8. Zofunika Pampingo
(7 min.)
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 2, mawu ofotokoza chigawo 2 komanso mutu 3