Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w24 November tsamba 32
  • Muzipeza Malo Abwino Ophunzirira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzipeza Malo Abwino Ophunzirira
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndingatani Kuti Maganizo Anga Azikhala pa Zimene Ndikupanga?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi N’kulakwa Kufuna Kuchitako Zinthu Zina Pandekha?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizikhala ndi Mpata Womachita Zinthu Pandekha?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi n’kulakwa kuchita zinthu zina pandekha?
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
w24 November tsamba 32

MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA

Muzipeza Malo Abwino Ophunzirira

Kodi mukufuna muzipindula kwambiri mukamaphunzira panokha? Mungayese mfundo zotsatirazi:

  • Muzisankha malo abwino. Ngati n’kotheka, muzipeza malo aukhondo komanso pamene pali kuwala kokwanira. Mukhoza kugwiritsa ntchito desiki kapena tebulo apo ayi mutha kupeza malo abwino alionse panja.

  • Muzikhala panokha. Yesu anasankha kukapemphera “m’mawa kwambiri” komanso “kumalo kopanda anthu.” (Maliko 1:35) Ngati n’zosatheka kukhala panokha, mungathe kuuza anthu a m’banja lanu kapena amene mumakhala nawo nthawi imene mumaphunzira, n’kuwapempha kuti asakusokonezeni.

  • Muziika maganizo pa zimene mukuphunzira. Muzipewa zinthu zimene zingakusokonezeni. Ngati mumagwiritsa ntchito foni kapena tabuleti pophunzira, muziitchera m’njira yoti isakusokonezeni. Mukaganizira zinthu zina zoti muchite, muzingolemba mwachidule penapake kuti mudzazichite nthawi ina. Ngati mukuona kuti maganizo anu ayamba kuyendayenda mukhoza kupuma kaye, kuyenda pang’ono kapena kudziwongolawongola.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena