Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb15 tsamba 170
  • Ndinkafuna Kusiya Kutumikira Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndinkafuna Kusiya Kutumikira Mulungu
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • Nkhani Yofanana
  • Umphawi Komanso Vuto Losowa Pokhala Zidzatha
    Galamukani!—2015
  • N’chifukwa Chiyani Wansembe Anasiya Chipembedzo Chake?
    Galamukani!—2015
  • Ndinasiya Kupita Kuchipembedzo Chilichonse
    Baibulo Limasintha Anthu
  • Yehova Wandichitira Zazikulu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
yb15 tsamba 170
Chithunzi patsamba 171

DOMINICAN REPUBLIC

Ndinkafuna Kusiya Kutumikira Mulungu

Martín Paredes

  • CHAKA CHOBADWA 1976

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1991

  • MBIRI YAKE Martin anaphunzira za Yehova nthawi yomwe ankachita maphunziro aunsembe. Kuyambira nthawi imeneyi iye wathandiza anthu ambiri kuti azitumikira Yehova.

Picture on page 170

NDINAKULIRA m’banja lachikatolika lokonda kupemphera kwambiri ndipo makolo anga ankafunitsitsa kuti ndidzakhale wansembe. Ndiyeno ndili ndi zaka 12 ndinachita maphunziro atatu ndipo ndinaphunzitsidwa ndi ansembe osiyanasiyana. Mu 1990, ndili ndi zaka 14, ndinaitanidwa kuti ndikachite maphunziro pasukulu inayake yapamwamba kwambiri yophunzitsa za unsembe.

Zinkandiyendera kwambiri moti anandiuza kuti ngati ndingapitirize kuchita khama ndidzakhala bishopu. Koma ndinakhumudwa chifukwa m’malo mophunzira Baibulo tinkaphunzira nzeru za anthu. Ansembenso anali achiwerewere moti ankafuna kuti agone nane. Zimenezi zinkandipangitsa kufuna kusiya kutumikira Mulungu.

Tsiku lina munthu wina wogwira ntchito pasukulupo anapatsidwa buku la Achichepere Akufunsa ndi amishonale. Ndinabwereka bukulo ndipo ndinaliwerenga lonse. Kenako ndinadziuza kuti: “Izi ndi zimene ndinkafuna.” Ndinachoka pasukulupo ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova kenako ndinayambanso kufika pamisonkhano. Ndiyeno mu July, 1991, patha miyezi 8 ndinabatizidwa. Kenako ndinayamba kuchita upainiya ndipo ndinakwatira Maria yemwe analinso mpainiya. Kuyambira mu 2006, takhala tikutumikira limodzi monga apainiya apadera. Sindifunanso zosiya kutumikira Mulungu ndipo ndikusangalala kuthandiza anthu kudziwa bwino Mulungu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena