Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 114
  • Ndingatani Ngati Ndili Ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndingatani Ngati Ndili Ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Bwanji Ndingodzipha?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Kodi Ndingatani Ngati Ndili ndi Matenda Ovutika Maganizo?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi ndingodzipha?
    Galamukani!—2008
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 114
Mtsikana amene akuvutika maganizo akuyang’anitsitsa panja pa windo pomwe pakugwa mvula.

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Ndingatani Ngati Ndili Ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?

“Zaka zapitazo, ndinkalimbana ndi nkhawa kwambiri moti zinkangokhala ngati kuti tsiku lililonse ndili pa chintchito chothimitsa moto. Nthawi imeneyo ndinkangoganizira zodzipha. Sikuti ndinkafunadi kufa, koma ndinkangofuna kuthana ndi mavuto omwe ndinkakumana nawo.”—Jonathan, wazaka 17.

Pa kafukufuku wina amene anachitidwa pa achinyamata 14,000 a kukoleji, pafupifupi wachinyamata mmodzi pa 5 aliwonse anavomera kuti anaganizapo zofuna kudzipha.a Kodi mungatani ngati nanunso mumaona kuti bola kungodzipha?

  • Dekhani. Tsimikizani mtima kuti simudzachita zinthu mopupuluma. Ngakhale kuti ndi zoona kuti mavuto omwe mukukumana nawo angaoneke aakulu kwambiri, pali njira zomwe mungatsatire kuti muthane nawo.

Mtsikana ali mumpanda wazipindazipinda ndipo akufufuza khomo loti atulukire.

Mukhoza kumaganiza kuti palibenso zomwe mungachite ndi mavuto omwe mukukumana nawo. Koma si nthawi zonse pomwe zomwe timaganiza zimakhaladi zolondola. Njira zothanirana ndi mavuto anu zilipo, ndipo ngati mutapeza thandizo loyenera, zinthu zikhoza kuyamba kuyenda bwino mwamsanga kuposanso mmene mukuganizira.

  • Mfundo ya m’Baibulo: “Timapanikizidwa mwamtundu uliwonse, koma osati kupsinjidwa moti n’kulephera kusuntha. Timathedwa nzeru, koma osati mochita kusoweratu pothawira.”—2 Akorinto 4:8.

    Zomwe mungachite: Ngati mukumangoganizira zodzipha, gwiritsani ntchito njira zomwe zilipo kuti mupeze thandizo. Mwachitsanzo, mungaimbire achipatala. Ogwira ntchito zachipatala, anaphunzitsidwa ndi cholinga choti akuthandizeni ndipo ndi ofunitsitsa kukuthandizani.

  • Lankhulani ndi winawake. Pali anthu omwe amakukondani omwenso ndi ofunitsitsa kukuthandizani. Anthuwa ndi monga anzanu komanso achibale anu omwe pawokha sangadziwe zomwe mukukumana nazo pokhapokha mutawauza.

Mtsikana wavala magalasi.

Anthu ena amaona zinthu bwinobwino akavala magalasi. Anthu ena nawonso angakuthandizeni kuti muyambe kuona zinthu moyenera komanso kuti musinthe maganizo n’kuyamba kuona moyo wanu kukhala wofunika.

  • Mfundo ya m’Baibulo: “Bwenzi lenileni . . . ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

    Zomwe mungachite: Kuti muyambe kukambirana, munganene kuti: “Masiku amenewa ndikumavutika maganizo ndi zinazake. Mungakonde kuti ndikuuzeni?” Kapena mukhoza kunena kuti: “Ndikulimbana ndi mavuto enaake omwe ndikuona kuti sindingathe kuthana nawo pa ndekha. Mungandithandizeko?”

  • Kaonaneni ndi adokotala. Matenda a nkhawa kapena ovutika maganizo akhoza kuchititsa munthu kuona kuti palibenso chifukwa chokhalira ndi moyo. Koma chosangalatsa n’chakuti mankhwala a matenda amenewa alipo.

Mtsikana yemwe akudwala akuyang’ana mothedwa nzeru. Amuikira chakudya pambali pake koma sakudya.

Monga mmene chimfine chimachititsira kuti munthu asakhale ndi chilakolako chofuna kudya, matenda ovutika maganizo amachititsanso munthu kuti asamasangalale ndi moyo. Komabe, matenda onsewa ali ndi mankhwala ake.

  • Mfundo ya m’Baibulo: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.”—Mateyu 9:12.

    Zomwe mungachite: Muzigona mokwanira, kuchita masewera olimbitsa thupi komanso kudya chakudya chopatsa thanzi. Ngati thupi lanu si lathanzi, zingakhalenso zovuta kuti muziganiza bwino.

  • Muzipemphera. Baibulo limanena kuti Mlengi wathu “ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” (1 Yohane 3:20) Pezani mpata woti mupemphere kwa iye. Popempherapo, tchulani dzina lake lakuti Yehova ndipo muuzeni zonse zomwe zili mumtima mwanu.

Mtsikana wanyamula chibokosi chachikulu movutikira.

Mavuto ena ali ngati chikatundu cholemera chomwe simungathe kunyamula nokha. Mulungu wanu Yehova, ndi wokonzeka kuti akuthandizeni.

  • Mfundo ya m’Baibulo: “Zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”—Afilipi 4:6, 7.

    Zomwe mungachite: Kuwonjezera pa kuuza Yehova za mavuto anu, tayesani kuganizira chinthu chimodzi chabwino chomwe mungamuthokoze nacho. (Akolose 3:15) Kukhala ndi mtima woyamikira, kungakuthandizeni kuti muziganizira zinthu zabwino ndipo zimenezi zingakuthandizeni kukhala ndi chiyembekezo.

Mukayamba kuona kuti moyo ulibenso phindu, ndi bwino kupempha ena kuti akuthandizeni. Zimenezi ndi zomwe Jonathan amene tamutchula kumayambiriro kwa nkhaniyi anachita. Iye ananena kuti: “Nthawi zambiri ndinkakambirana ndi makolo anga komanso ndinapita kuchipatala kukalandira chithandizo. Koma panopo ndikupezako bwino. Ngakhale kuti nthawi zina ndimakhumudwabe ndi zinthu zina, sindikhalanso ndi maganizo ofuna kudzipha.”

a Kafukufukuyu anachitika mu 2019 ndi a U.S. Centers for Disease Control and Prevention.

Zimene achinyamata anzanu amanena

Alexandra.

“Kukhala ndi maganizo angwiro ndi kofunika kwambiri mofanana ndi kukhala ndi thupi lathanzi. Kungoti kusiyana kwake n’kwakuti, munthu akathyoka mkono kapena mwendo zimaonekera mosavuta. Koma zimakhala zovuta kudziwa ngati munthu wina akuvutika maganizo. Ngati muli ndi vutoli, muzimasuka kuuzako winawake. Zimakhala bwino kwambiri kupempha munthu wina kuti akuthandizeni.”—Alexandra.

Ian.

“Ndimakumbukira zomwe makolo anga anandiuza ndili mwana, kuti palibe vuto lomwe ndi losatheka kulithetsa kapena lomwe munthu sangathe kulipirira. Kupeza munthu amene ukhoza kumamuuza nkhawa zako ndi kothandiza. Mwachitsanzo, ineyo makolo anandithandiza kwambiri kuti ndiziona moyenera mavuto omwe ndinkakumana nawo.”—Ian.

Mavesi a m’Baibulo omwe angakuthandizeni

Lembani mavesi angapo a m’Baibulo omwe angakuthandizeni pa nthawi imene mwavutika maganizo. Mungayambe ndi mavesi otsatirawa.

Salimo 34:18: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”

Tanthauzo lake: Yehova amasamala kwambiri za anthu amene amaona kuti mavuto awo ndi aakulu ndipo alibiretu mtengo wogwira. Iye amafuna kuwathandiza.

Salimo 46:1: “Mulungu ndiye pothawira pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.”

Tanthauzo lake: Mungathe kupemphera kwa Yehova nthawi iliyonse imene muli ndi nkhawa. Iye ndi wokonzeka komanso wofunitsitsa kukuthandizani kuti muthe kupirira.

Salimo 94:18, 19: “Pamene ndinanena kuti: “Phazi langa literereka,” kukoma mtima kwanu kosatha, inu Yehova, kunandichirikiza. Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, Mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”

Tanthauzo lake: Mulungu angakutonthozeni mukamawerenga Mawu ake Baibulo. Ndipo musamalole kuti tsiku lidutse musanawerenge Mawu ake.

Salimo 139:23, 24: “Ndifufuzeni, inu Mulungu, . . . ndi kudziwa malingaliro anga amene akundisowetsa mtendere, ndipo muone ngati mwa ine muli chilichonse chimene chikundichititsa kuyenda m’njira yoipa, ndipo munditsogolere m’njira yamuyaya.”

Tanthauzo lake: Yehova amakudziwani bwino kwambiri kuposa mmene mumazidziwira. Iye angakuthandizeni kuchotsa maganizo aliwonse oipa kuti muyambirenso kukhala wosangalala.

Yesaya 41:10: “Usachite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.”

Tanthauzo lake: Kaya tikukumana ndi mavuto otani, Yehova angatipatse mphamvu kuti tithe kupirira.

Mfundo zachidule: Ndingatani Ngati Ndili Ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?

  • Dekhani. Tsimikizani mtima kuti simudzachita zinthu mopupuluma. Pali njira zomwe mungatsatire kuti muthane ndi mavuto omwe mukukumana nawo.

  • Lankhulani ndi winawake. Anzanu komanso achibale anu, sangadziwe zomwe mukukumana nazo pokhapokha mutawauza.

  • Kaonaneni ndi adokotala. Kufuna kudzipha kungakhale chizindikiro cha matenda ovutika maganizo. Komabe matendawa ali ndi mankhwala ake.

  • Muzipemphera ndi kuuza Mulungu maganizo anu. Iye amakudziwani bwino kwambiri kuposa mmene mumazidziwira ndipo amafuna kukuthandizani.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena