Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt tsamba 2214-2215
  • B1 Uthenga wa MʼBaibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • B1 Uthenga wa MʼBaibulo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chaka cha 4026 B.C.E. Chitadutsa
  • Mu 1943 B.C.E.
  • Chaka cha 1070 B.C.E. Chitadutsa
  • Mu 29 C.E.
  • Mu 33 C.E.
  • Cha mʼma 1914 C.E.
  • Mʼtsogolo
  • Ulosi Wakalekale Umene Umakukhudzani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Mulungu Anaulula Cholinga Chake
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Mbewu ya Njoka—Yavumbulidwa Motani?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kugwirizana kwa Baibulo Lonse
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
Onani Zambiri
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
B1 Uthenga wa MʼBaibulo

B1

Uthenga wa MʼBaibulo

Losindikizidwa

Yehova Mulungu ndi amene ali woyenera kulamulira ndipo ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. Cholinga chake chokhudza dziko lapansi ndi anthu chidzakwaniritsidwa.

Adamu ndi Hava ali mʼmunda wa Edeni, ndipo njoka ili mumtengo chapafupi

Chaka cha 4026 B.C.E. Chitadutsa

“Njoka” inakayikira zoti Yehova ndi wolamulira wabwino. Yehova analonjeza kuti padzakhala “mbadwa ” kapena “mbewu” imene mʼkupita kwa nthawi idzaphwanya mutu wa njoka yomwe ndi Satana. (Genesis 3:1-5, 15, mawu amʼmunsi) Komabe Yehova walola kuti anthu adzilamulire motsogoleredwa ndi mphamvu ya “njoka.”

Abulahamu akumvetsera lonjezo la Mulungu

Mu 1943 B.C.E.

Yehova anauza Abulahamu kuti “mbadwa” yolonjezedwa idzachokera mwa ana ake.—Genesis 22:18.

Mfumu Davide

Chaka cha 1070 B.C.E. Chitadutsa

Yehova anatsimikizira Mfumu Davide, kenako anatsimikiziranso mwana wake Solomo, kuti “mbadwa” yolonjezedwayo idzachokera mʼbanja lake.—2 Samueli 7:12, 16; 1 Mafumu 9:3-5; Yesaya 9:6, 7.

Yesu pa nthawi imene ankabatizidwa

Mu 29 C.E.

Yehova anasankha Yesu kukhala “mbadwa” yolonjezedwa kuti adzakhale pampando wachifumu wa Davide.—Agalatiya 3:16; Luka 1:31-33; 3:21, 22.

Yesu pa nthawi imene ankaphedwa

Mu 33 C.E.

Pofuna kulepheretsa kuti pasakhale “mbadwa” yolonjezedwa, Satana, yemwe ndi njoka, anapha Yesu. Koma Yehova anaukitsa Yesu yemwe kenako anapita kumwamba. Kumeneko Yehova analandira moyo wangwiro wa Yesu, womwe umathandiza kuti anthu azitha kukhululukidwa machimo ndiponso kuti mbadwa za Adamu zidzalandire moyo wosatha.—Genesis 3:15; Machitidwe 2:32-36; 1 Akorinto 15:21, 22.

Njoka, yomwe ndi Satana akuponyedwa padziko lapansi monga mmene zinalonjezedwera mʼbuku la Chivumbulutso

Cha mʼma 1914 C.E.

Yesu anaponya njoka, yemwe ndi Satana, padziko lapansi kuti akhalepo kwa kanthawi kochepa.—Chivumbulutso 12:7-9, 12.

Yesu wakhala pampando wachifumu akulamulira dziko lapansi monga mmene zinalonjezedwera mʼbuku la Chivumbulutso

Mʼtsogolo

Yesu adzamanga Satana kwa zaka 1,000, kenako adzamuwononga, zomwe zikuimira kuphwanya mutu wa Satana. Ndiyeno cholinga choyambirira cha Yehova chokhudza dziko lapansi ndi anthu chidzakwaniritsidwa. Dzina lake lidzayeretsedwa ndipo zimenezi zidzasonyeza kuti iye ndi woyenera kulamulira.—Chivumbulutso 20:1-3, 10; 21:3, 4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena