Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 10/8 tsamba 6-7
  • Bwanji Ponena za Umoyo Wabwino wa Inu Eni?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bwanji Ponena za Umoyo Wabwino wa Inu Eni?
  • Galamukani!—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Umoyo Wabwino Kaamba ka Onse—Chofunika Chachikulu
    Galamukani!—1987
  • Magwero Apamwamba Kwambiri a Nzeru
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Kodi Mulungu Amaona Kuti N’kulakwa Kusuta Fodya?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Sungirirani Chikhulupiriro Chanu ndi Umoyo Wauzimu
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Galamukani!—1987
g87 10/8 tsamba 6-7

Bwanji Ponena za Umoyo Wabwino wa Inu Eni?

MANKHWALA amayesa kuchiritsa matenda. Kaŵirikaŵiri amapambana kuchita tero, koma khalidwe la umoyo wabwino la moyo likanachinjiriza matenda panthaŵi yoyamba.

Dr. Halfdan Mahler, mtsogoleri wa mayanjano aunyinji wa WHO, wanena kuti tifunikira kuyamba mathayo a umoyo wabwino wa ife eni, “kudya mwanzeru, kumwa pang’ono, kusasuta, kuyendetsa magalimoto mosamalitsa, kuchita masewera mokwanira, kuphunzira kukhala pansi pa vuto la umoyo wa m’mizinda, ndi kuthandizana wina ndi mnzake kuchita tero.”

Baibulo ndi uphungu wake wanzeru ndi kuweruza kwabwino lingatithandize ife mokulira pa nkhaniyi. Malamulo ake amatsogolera ku moyo wabwino kwambiri ndipo mwakutero ku umoyo wabwino mu dziko lathu lovuta. Kuphunzitsa kwake kuli “mawu a moyo” osati kokha mu lingaliro la kuuzimu komanso m’lingaliro la kuthupi. Zonena zake zabwino ziri “moyo kwa omwe adzipeza nalamitsa thupi lawo lonse.”—2 Timoteo 1:13; Miyambo 4:22.

Koma ngakhale kuposerapo, malamulo a Baibulo angachepetseko kuwopsya kwa mavuto odzetsa imfa. Kodi zimenezo ziri zothekera motani? Pano pali zitsanzo zina:

Boma la U.S. limatcha kusuta kwa ndudu kukhala “mwachiwonekere chochititsa chachikulu chimodzi chokhoza kuchinjirizidwa cha kudwala ndi imfa ya mwamsanga mu United States.” Nthenda za kansa zapambana nthaŵi zisanu ndi imodzi pakati pa amuna omwe amasuta kuposa omwe sasuta. Baibulo limati: “Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu.” (2 Akorinto 7:1) Mboni za Yehova zagwiritsiranso ntchito ichi kwanthaŵi yaitali ku kusuta fodya. Chotero, kwa iwo eni achepetsa mokulira chochititsa chimodzi chachikulu cha nthenda zochititsa mantha zadziko.

Kugwiritsira ntchito molakwa zakumwa zoledzeretsa ndi kuledzera sikumangochititsa kulimbitsa timitsempha tachiwindi komanso kumenyana, kukangana, chiwawa, ndi mliri watsopano wa ngozi za magalimoto zodzetsa imfa. Kodi Baibulo lingathandize pano?

Ilo limalangiza kuchepetsako kugwiritsira ntchito zakumwa zoledzeretsa, likumati: “Kapena oledzera, kapena olalatira, . . . sadzalowa Ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere.” Ndiponso: “Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru.” (1 Akorinto 6:9-11; Miyambo 20:1) Kodi uphungu wa umoyo wa Baibulo umenewu umapanga nzeru zabwino?

Kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka a narcotic kwakhala vuto loipa la umoyo wabwino pakati pa achichepere amakono. Health Crisis 2000 imati: “Ndalama zambiri zimawonongedwa pa kuchirikiza lamulo molimbana ndi kugwiritsira ntchito kofala kwa anamgoneka pamene kuli kwakuti zochepa zimawonongedwa pa kuchinjiriza achichepere athu osalimba ku kukhala omwerekera pa nthaŵi yoyambirira.” Mboni za Yehova zimagwiritsira ntchito ku anamgoneka osokoneza maganizowa malamulo amodzimodzi ozikidwa mu Baibulo omwe amagwira ntchito ku fodya. (2 Akorinto 7:1) Makolo amawonetsa chitsanzo mu nkhaniyi, kuchiphunzitsa icho kwa ana awo, ndipo ichi chimapita patali pa kuchinjiriza kumwerekera poyambirira.

Matenda opatsirana mwa kugonana, onga ngati chinzonono ndi AIDS, ali chiwopsyezo chowonjezereka kwa anthu omwe amakhala ndi mabwenzi ogonana nawo ambiri. Kodi Baibulo limanenanji ponena za ichi? Ilo momvekera bwino limatsutsa chisembwere. Ilo limaphunzitsa kukwatira munthu mmodzi kwa moyo wonse ndipo kukhala wokhulupirika mwa makhalidwe kwa munthuyo. Ilo limati: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.” (Ahebri 13:4) Ndiponso, ilo limati: “Ndipo ntchito za thupi ziwonekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, . . . iwo akuchita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.”—Agalatiya 5:19-21; Mateyu 5:32.

Malamulo a Baibulo abwino oterewa amatsogolera ku umoyo wabwino ngakhale mu dziko lodzala ndi mavuto lamakono, koma sangapereke kuchiritsa kosatha. Kuchiritsa kosatha liri phunziro la nkhani yotsatira.

[Zithunzi patsamba 7]

“Taika mabala pa ife tokha, m’kukhulupirira kuti sayansi, adokotala ndi zipatala zingapeze chochiritsa, m’malo mochinjiriza zochititsa zenizeni za kudwala poyamba.”—Health Crisis 2000

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena