Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 10/8 tsamba 24-25
  • Akasupe a Moto a ku Hawaii

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akasupe a Moto a ku Hawaii
  • Galamukani!—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuphulika kwa Dzawoneni
  • Chiphunzitso cha Chihawaii
  • Chochitika cha Posachedwapa cha Matanthwe a Pansi Panthaka
  • N’chifukwa Chiyani Chimatchedwa Chilumba Chachikulu?
    Galamukani!—2008
  • Mmene Tinapulumukira Zoopsa Phiri Litaphulika N’kumatuluka Chiphalaphala!
    Galamukani!—2002
  • Kukhala Pafupi ndi Chimphona Chimene Chili M’tulo
    Galamukani!—2007
  • “Chokani Tsopano!”
    Galamukani!—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—1987
g87 10/8 tsamba 24-25

Akasupe a Moto a ku Hawaii

MULI utsi wofiira mthambo la usiku, kununkha koipa m’mpweya, ndipo maso a wina awaŵidwa kaamba ka kuipitsidwa kwa mphepo. Kodi nchiyani chikuchitika? Nchifukwa ninji anthu akukonzekera kaamba ka kuthekera kwa kuchoka m’nyumba zawo? Kodi uli moto wa ku nkhalango? Ayi, kusokonezeka kwachititsidwa ndi matanthwe otentha a pansi pa nthaka, okhalanso ndi mphamvu ndipo kachiŵirinso kumachititsa dzawoneni wa kusonyeza kwa moto.

Kuphulika kwa matanthwe otentha a pansi pa nthaka pa “Chisumbu Chachikulu” mu Hawaii kuli moposerapo chochitika chofala. Mwachitsanzo, matanthwe otentha a pansi pa nthaka a ku Kilauea, akhala ndi mbali 48 za kugwira ntchito kuchokera pamene anayamba kuphulika pa January 3, 1983. Nthaŵi zambiri mbali zimenezi zimatenga maora 24 kapena kucheperapo ndipo zimakhala ndi akasupe athope omwe amachokera pa mapazi mazana angapo kufika ku chifupifupi chikwi chimodzi kutalika kwake, okhala ndi matope oyenda kufalikira ku mamailosi angapo kuchokera ku malo ake otulukira.a

Kuphulika kwa Dzawoneni

Kuphulika kwa mu ngululu ya 1984, ngakhale ziri tero, kunali kosiyana. Nthaŵiyi, Mauna Loa—matanthwe otentha a padziko lapansi achangu padziko lonse, okhala ndi mlingo wa mapazi 33,000 kuchokera mu nthaka ya m’nyanja kufika ku mlingo wakutali—anadzakhalanso ndi moyo. Chiyambire kuphulika kochepa kwa tsiku limodzi mu July 1975, Mauna Loa akafunikira kukhala wachangu masiku 22 mkati mwa March ndi April. Ilo linabzikula avereji yoposa pa 1.3 miliyoni cubic yards ya thope pa ora limodzi nthaŵi yonseyo.b Izo ndizo zinthu zokwanira za matanthwe otentha a pansi pa nthaka zoponyedwa kunja mu ora limodzi lokha kuyala ukulu wa mainchi anayi, mapazi anayi mu ukulu mtunda wonsewo kuchokera ku Honolulu kufika ku New York, mtunda wa mamailosi 4,873!c

Mlingo wokulira wamatope unapangitsa matope oyenda osiyanasiyana. Ena a iwo anayenda moloza ku Hilo, mzinda waukulu pa chisumbupo, wokhala ndi chiŵerengero cha anthu oposa pa 35,000. Olamulira anayang’anitsitsa pa mkhalidwewo, ndipo kudera nkhaŵa kunafikira chiŵerengero chachikulu pamene mtsinje waukulu wa matope unayenda kufika ku mamailosi asanu a mzinda. Koma pamene zinthuzo zinachitika, panalibe kuwopsyeza konunkha kanthu ku moyo kapena ku chuma mosasamala kanthu za matope onsewo otulutsidwa.

Pamene Mauna Loa ankaphulika, Kilauea nayenso anayambanso mochepera, wokhala ndi matope akumayenda kufika pa utali wa chifupifupi mapazi 700. Ichi chinapangitsa mkhalidwe wosakhala wanthaŵi zonse wa matanthwe otentha a pansi pa nthaka aŵiri amphamvu akumaphulikira pamodzi pa chisumbucho—nthaŵi yoyamba chiyambire 1868 pamene ichi chinachitika.

Chiphunzitso cha Chihawaii

Monga mmene zingayembekezedwere, kusonyeza kwa chibadwa kowopsya kumeneko kumaitanira mwambo ndipo nthaŵi zina kuyankha kokhulupirira malaulo kuchokera kwa anthu. Chiphunzitso cha Chihawaii chimanena kuti matanthwe otentha a pansi pa nthaka ali mudzi wa mulungu wachikazi wa moto wotchedwa Pele ndi kuti pamene matanthwe otentha a pansi pa nthaka akuwopsyeza moyo kapena chuma, iye akusonyeza mkwiyo wake. Panthaŵi zoterozo, okhala ku Hawaii akale ankapereka zakudya ndi zakumwa monga nsembe za kufuna kukondweretsa Pele.

A Hawaii amakono ena akumamatirabe ku ina ya miyambo imeneyi. Mkati mwa kuphulika kwa mu 1984 kwa Mauna Loa, chifupifupi kahuna mmodzi, kapena mtsogoleri wa chipembedzo wa ku Hawaii, anachitiridwa ripoti kukhala akutsikira ku mapiri ku malo otulukirako matopewo kukapereka nsembe za nsomba zofiira ndi mizu ya taro ku mulungu wachikazi wa motoyo, Mama Pele.

Chiphunzitso cha Chihawaii chinafalikiranso mkati mwa nthaŵi ya kuphulika kuŵiri kwa Mauna Loa ndi Kilauea. Mkati mwa usiku, anthu ambiri, kuphatikizapo ogwira ntchito a ku National Park Service, anasimbidwa kukhala atawona kuphimba koyera mthambo, kotsagana ndi kung’anima kwakukulu kowala. Kulingana ndi chiphunzitso cha Chihawaii, ichi chinalongosoledwa kuti anali Pele yemwe anali kuyenda mu choyendera chake cha moto, kapena popoahi, akumayenda kuchokera ku thanthwe limodzi lotentha la pansi pa nthaka kufika ku linzake m’malo mofuna kutsimikiza ufumu wake.

Chochitika china chinachitikanso mkati mwa zochitika zamatanthwe otentha a pansi pa nthaka. Chipale chofewa, chochititsidwa ndi mikhalidwe ya chibadwa pamwamba pa Mauna Loa, chinagwa mwakamodzikamodzi pa phiri mkati mwa kuyenda kwa matope ake. Pamene asayansi ankalongosola mmene utsi ndi phulusa zofalikira m’mpweya zikathandizira kupanga chipale chofewacho aja ozolowerana ndi chiphunzitso cha Chihawaii anali ndi kulongosola kwina kwake.

Kulingana ndi chiphunzitsocho, kugwa kwa chipale chofewa pa matanthwe otentha a pansi pa nthaka kukakhala umboni wa milungu yachikazi iŵiri—Pele ndi mng’ono wake Lilinoe, mulungu wachikazi wa chipale chofewa—akumamenyerana kaamba ka ufumu wawo, Mauna Loa. Chenicheni chakuti chipale chofewacho chinasungunuka mwamsanga chitangofika pa matopewo chikatanthauza kuti Pele anapambana kumenyanako mu kulimbanira ufumu.

Chochitika cha Posachedwapa cha Matanthwe a Pansi Panthaka

Mauna Loa wakhala chete chiyambire 1984, koma Kilauea, yemwe wakhala ndi nyengo zophulika 48 chiyambire January 1983, anasinthira kukhala kuthira kopitirizabe kwa matope pa July 18, 1986. Kuthira kwa tsiku ndi tsiku koposa theka la mtunda wa miliyoni imodzi ya cubic yards wa thanthwe losungunuka unafikira ku nyanja November yapita. Mtsinje wa thope wotalika mamailosi asanu ndi atatu, womwe unavutitsa Kalapana Highway, unawonjezera dziko latsopano ku mtunda wa ku gombe, koma unawononga nyumba 26 podzafika mu December, ndi zina 80 zomwe zikali kuwopsyezedwabe.

Pamene kuli kwakuti matanthwe otentha a pansi pa nthaka a ku Hawaii akhala osavulaza mwachisawawa, kwakhala kuwonongeka kolinganizidwa kwa zinthu posachedwapa. Pamakhala ngozi yochepa ku moyo, pamene matanthwe otentha a pansi pa nthaka ndi matope ake ayenda m’mbali za kutali. Matope atayamba kuyenda kufupi ndi malo okhalako anthu, olamulira akhala okhoza kupereka chenjezo lokwanira lapasadakhale kuti alole kaamba ka kuchoka kwa ubwino ndi kwa dongosolo.

Matanthwe otentha a pansi pa nthaka achita mbali yawo yaikulu m’kukonzekeretsa dziko lapansi kaamba ka kukhalapo kwa mtundu wa anthu, ndipo achita zambiri ku kulemeretsa nthaka ndi kukonza bwino mbali zake. Kuwopsya kwadzawoneni kwa akasupe a moto a ku Hawaii kungawonedwe mopanda mantha a kukhulupirira malaulo. M’malo mwake, tikufulumizidwa kupereka ulemerero kwa Yehova, Mulungu wa chilengedwe chonse.

[Mawu a M’munsi]

a 1 ft = 0.3 m; 1 mi = 1.6 km.

b 1 cu yd = 0.76 cu m.

c 1 in. = 2.5 cm.

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

National Park Service photos

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

National Park Service photo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena