Kuŵerenga Mofuula Kumapangitsa Kuphunzira Kukhala Kosangalatsa
“CHACHIŴIRI ku kukupatira mwana wanu,” akutero Jim Trelease, mkonzi wa The Read-Aloud Handbook, mpatseni mwana wanu “mbali ya maganizo anu ndi mbali ya nthaŵi ya-nu.”
Motani? Mwakuŵerenga mofuula kwa iye koyambirira m’moyo wake ndipo kaŵirikaŵiri akuvomereza Trelease. Chokumana nachocho ndi mapindu amene inu ndi mwana wanu mudzalandira ali osatha. M’njira zotani? Sikuti kokha kuŵerenga koteroko kudzabweretsa zikumbukiro zanu za nthaŵi zosangalatsa kwambiri pambuyo pa kukula kwamwanayo koma zidzathandiza mwana wanu kukhala m’ŵerengi wabwino ndi wophunzira wabwinonso. Mwana wanu adzakulitsanso luso la kupenya chifukwa iye adzakhala akuphunzira kulunjikitsa chidwi chake pa chithunzithunzi. Mwachitsanzo, pa miyezi 18 mwana angakhoze kuzindikira chithunzithunzi cha kagalu kakang’ono, ndipo iye angamvetsetse liwulo mwamsanga kwambiri asanayambe kuliŵerenga ilo. M’kuwonjezerapo, osati kokha kuŵerenga, kulemba, kulankhula, kumvetsera, ndi maluso akulingalira a mwana wanu adzakulitsika komanso kawonedwe kake kulinga ku kukhala m’ŵerengi wabwino kadzawongoleredwanso—iye adzasangalala ndi kuŵerenga.
“Ndikuti kumene ndidzapeza nthaŵi kapena mphamvu ya kuŵerenga mofuula kwa ana anga?” Ndi kulira komvedwa kaŵirikaŵiri kwa makolo odandaula.
Jim Trelease akuwona kuti: “Tate amene amanena kuti ali wotopa kwambiri kuŵerenga kwa ana ake amagwiritsira ntchito maso aŵiri omwewo kuwonera wailesi ya kanema.”
Kuti apange masinthidwe m’kawonedwe kameneka, mkonzi Trelease akugawana nsonga izi ndi makolo oŵerenga amtsogolo:
1. Ŵerengani mabukhu abwino. Ana ambiri sakonda mabukhu amene amalalikira kwa iwo. Koma amasangalala ndi nkhani zokhala ndi mkangano kapena mavuto oti alakidwe. Tsimikizirani, ngakhale kuli tero, kuti mwanayo ali wokonzekera mwamaganizo kaamba ka bukhulo mwa kuwoneratu ilo inu eni.
2. Tengani nthaŵi yabwino koposa. Kuŵerenga kwa mwana wanu m’mawa kwambiri, pamene iye ali womangika, mwinamwake siiri nthaŵi yabwino koposa. Ena amaŵerenga kwa ana awo pamene iye wakhazikitsidwa pa mpando wautali kapena akudya. Yokondedwa kwambiri iri nthaŵi yogona. Mwanayo kenaka amakhala ndi nthaŵi yotalikirapo ya chisamaliro.
3. Kumanani ndi chitokoso. Palibe kuvulaza kulikonse m’kuŵerenga bukhu lokhala ndi mawu a akulu oposa kumvetsetsa kwa mwanayo. Kholo lingapereke tanthauzo lopepuka la liwulo, kuligawanitsa ilo, kapena ngakhale kudumpha mbali zovuta.
4. Gwiritsirani ntchito maluso anu akuŵerenga. Kuŵerenga mofuula kumaitanira kaamba ka kupuma kwabwino ndi liŵiro labwino. Ngati muli wokaikira ponena za kachitidwe kanu, jambulani nkhani pa tepi rekorda, iseŵereninso iyo, ndipo kenaka kambani maluso anu akuŵerenga.
5. Wonani utali wakumvetsera. Zowona, nkhani yabwino ingagwire chikondwerero cha mwana wanu, koma dziŵani kuti iye sangapereke chisamaliro chake chonse ku nkhaniyo. Komabe, iye adzaphunzira chinachake kuchokera ku iyo.
6. Khalani oleza mtima. Mofanana ndi achikulire ena omwe amasangalala ndi kuwona nkhani imodzimodziyo mobwerezabwereza, ana amafuna kumva nkhani yawo ya pamtima kwambiri ikuŵerengedwa mobwerezabwereza chifukwa iwo amazindikira matanthauzo atsopano nthaŵi iriyonse. Chotero m’malo mwa kuchotsa bukhu lapamtima, ingowonjezeraniko nkhani yatsopano.