Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 1/8 tsamba 22-24
  • Wopanda Nyumba—Koma Wamoyo!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Wopanda Nyumba—Koma Wamoyo!
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito ya Chithandizo mu Tokyo
  • Kulimbikitsidwa ndi Kudera Nkhaŵa kwa Ena
  • “Chokani Tsopano!”
    Galamukani!—1988
  • Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Kodi a Mboni za Yehova amagwira nawo ntchito yothandiza ena pakagwa tsoka?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Mmene Tingathandizire Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 1/8 tsamba 22-24

Wopanda Nyumba—Koma Wamoyo!

Ndi Mlembi wa “Galamukani!” mu Japani

MABWATO oyambirira onyamula anthu ochokera pa zisumbu anafika pa madoko mphepete mwa Izu Peninsula mkati mwa usiku wa November 21. Pambuyo pake chinalingaliridwa kuti anthuwa ayenera kutumizidwa ku Tokyo, popeza Oshima ali pansi pa ulamuliro wa boma lolamulira la Tokyo. Boma lolamulira limodzi ndi boma la mtundu linatenga mphamvu mkulinganiza ntchito ya chithandizo. Mboni za Yehova mmalo onse aŵiri a mu Izu ndi Tokyo limodzi ndi malikulu a nthambi, lokhala mu Mzinda wa Ebina kokha chifupifupi mamailosi 50 (80 km) kuchokera ku Phiri la Mihara, nawonso analinganiza ntchito ya chithandizo.

Popeza maripoti anyuzi a chochitikacho anasokoneza maprogramu okhazikika a wailesi ya kanema, Mboni za Yehova zokhala pafupi zinakhala zodera nkhaŵa mwapadera kaamba ka abale ndi alongo awo auzimu pa chisumbucho. Nobumasa Obata wa ku Mpingo wa Ito ndi ena anagwirizana ndi Mboni m’dera la Izu ndipo analinganiza ntchito yolandira anthu ochoka pa chisumbu. Pofika pa 6:30 p.m. tsiku limenelo, Mboni zinali pa doko lirilonse pa Izu Peninsula ndi Atami, zokonzekera kulandira abale awo ochokera ku Oshima.

Pamene Jiro Nishimura ndi ena anayi anafika pa Atami chifupifupi 10 koloko usiku umenewo, Mboni mu Atami, ndi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! m’manja mwawo, zinakumana ndi iwo. Popeza olamulira aboma anali asanalingalire zochita, anthu ochoka pa zisumbuwo analoledwa kukhala ndi munthu aliyense yemwe anafuna. Anapita ku Yugawara, kumene mwana wa Nishimura akutumikira monga mkulu mu mpingo wa kumaloko. Chipinda chomwe anali kukhala anakhala malo apakati owonera zomwe zikuchitika kwa aja ochoka ku zisumbu a Mpingo wa Oshima.

Pa 8:00 m’mawa wotsatira, Komiti ya Nthambi pa malikulu a nthambi ya Watch Tower Society mu Ebina analingalira kutumiza mwamsanga oimira nthambi aŵiri ku dera la Izu ndi aŵiri ku Tokyo kulinganiza ntchito ya chithandizo.

Pamene oimira nthambi anali kukambitsirana za ntchito yachithandizo ndi Nishimura, Mitsuo Shiozaki anafika ndi zoperekedwa zachithandizo kuchokera ku mpingo wake mu Numazu. Anthu ochoka kuchisumbuwo anayamikira makamaka zovala zomwe anawagawira pakati pawo, popeza ambiri a iwo analibe chovala chirichonse kusiyapo kokha zomwe anavala pamene anachoka pa chisumbu chawo. Anayamikiranso chakudya chomwe anawabweretsera.

Makomiti a chithandizo anasankhidwa mu Izu ndi Tokyo kugawira ndalama zofunika ku ziwalo za Mpingo wa Oshima. Makomiti oterowo anayeneranso kuyang’anira pa zosowa zauzimu za anthu ochoka pa zisumbuwo.

Ntchito ya Chithandizo mu Tokyo

Pa 9:55 p.m. pa November 21, pambuyo pakuchoka kwa zombo zina zochoka pa zisumbupo kupita ku mizinda pa Izu Peninsula, bwanankubwa wa ku Tokyo analamulira kuti anthu onse ochoka pazisumbu atumizidwe ku Tokyo. Yoshio Nakamura, mkulu mu Mpingo wa Mboni za Yehova wa Mita mu Tokyo, anafunsidwa kulinganiza kaamba ka ntchito yothandiza kumeneko. Nyumba ya Nakamura inakhala malikulu a ntchito yachithandizo mu Tokyo.

Anafunsa ena kuchokera mu mpingo wake ndi ena kuchokera mu mpingo wa Shinagawa kubwera ndi iye. Khumi a iwo anachoka pa nyumba ya Nakamura chifupifupi 2 koloko Loweruka m’mawa ndipo anapita pamsewu womangidwa ndi chitsulo pa nyanja kuchokera ku doko kumene mabwato ochokera ku Oshima anandandalitsidwa kufikirako. Abale anali okonzekera ndi zizindikiro zonena kuti: “Ziwalo za Mpingo wa Mboni za Yehova mu Oshima, chonde gwirizanani nafe.”

Kufikira pamene chombo chomaliza chinabwera, anali kuyenda kutsogolo ndi kumbuyo pakati pa misewu iŵiri yopangidwa ndi zitsulo pa nyanja kuchokera ku doko pomwe mabwato anali kufikira. Panali pambuyo pa 10 koloko Loŵeruka m’mawa. Mboni za Yehova mu mpingo wa Chuo zinapitanso pa msewu womangidwa ndi chitsulo pa nyanja kuchokera pa doko pomwe zombo zochokera ku Oshima zinafikira. Mosazindikira kuti ndi chombo chiti chomwe chingakhale ndi okhulupirira anzawo, Mboni mu Tokyo zinayesa kukumana ndi zombo zonse zomwe zinabwera ku Tokyo.

“Mboni za Yehova,” akumbukira Kazuyuki Kawashima, “zinali oimira gulu la chipembedzo okha omwe anabwera kudzalandira okhulupirira anzawo pamsewu womangidwa ndi chitsulo pa nyanja kuchokera pa doko. Gulu lina lokha lomwe linabwera kudzalandira anthu ochoka kuzisumbu linali la aphunzitsi.”

Kufika pa Loŵeruka madzulo, ziwalo za mpingo wa Mita ndi Shinagawa modzipereka zinasonkhanitsa zovala ndi zopereka zina za thandizo kaamba ka kugawiridwa kwa mwamsanga pakati pa abale awo auzimu ochokera ku Oshima. Mbonizo zinalonga zopereka zimenezi mu galimoto ndi kuchezera misasa imene Mboni zochoka pa zisumbu zinali kukhala. Mboni zochokera ku Oshima pamodzi ndi aja omwe sanali Mboni omwe anali kumeneko anapindula kuchokera ku thandizo limeneli.

Kulimbikitsidwa ndi Kudera Nkhaŵa kwa Ena

Mboni ina yochoka pa chisumbu inanena kuti: “Pamene tinachoka ku Oshima, ife eni sitinadziwe kumene tinali kupita. Pamene tinatuluka mu chombo, ngakhale kuli tero, tinawona chizindikiro chakuti, ‘Mboni za Yehova.’ Lingalirani mmene tinaliri odabwitsidwa ndi kukondweretsedwa! Misozi inatsika m’maso mwa mkazi wanga pamene anapambanidwa ndi mpumulo pa kupeza abale athu akumeneko kutilandira pa msewu womangidwa ndi zitsulo pa nyanja kuchokera pa doko.

“Mosachedwa pamene tinafika mu Sports Hall mu Koto Ward ndikutumiza foni kwa Mbale Nakamura ndi pamene oimira nthambi anafika kutilimbikitsa ife. Ichi ndithudi chinatikondweretsa ife, ndipo sitinapeze mawu aliwonse kusonyeza chiyamikiro chathu.”

Mkati mwa mlunguwo, ziwalo za komiti ya chithandizo zinachezera misasa yomwe kunali Mboni ndi kuwona zosowa za okhulupirira anzawo. Anapeza kuti Mboni zochoka pa chisumbu zinali kusamaliridwa bwino ndi mipingo ya kumaloko. Ophunzira Baibulo ena anaitanidwa kunyumba za Mboni za kumaloko kaamba ka chakudya cha tsiku lonse ndipo anayamikira kachitidwe kachikondi koteroko kosonyezedwa ndi Mboni zomwe sanazidziwe tsokalo lisanachitike.

Kuchoka kumeneku kunali kwachipambano chifukwa machenjezo oyenerera anapatsidwa ndipo anthu anawalabadira. Koma mtundu wonse wa anthu ukuyang’anizana ndi tsoka lalikulu lomwe likudza ndi liŵiro lalikulu. Chenjezo likupatsidwa tsopano, kusonyeza anthu mmene iwo angathaŵire tsoka limeneli ndi kupulumutsa miyoyo yawo. Kodi mudzalabadira chenjezo limeneli?

[Chithunzi patsamba 22]

Jiro Nishimura akufunafuna malo komwe okhulupirira anzake analia

[Mawu a M’munsi]

a Mboni ya Yehova yokondedwa kwambiri imeneyi inafa mu February 1987.

[Chithunzi patsamba 23]

Mitsuo Shiozaki akugawira zinthu zathandizo

Anthu ambiri omwe anathaŵa anagona pansi pozizira m’chipinda chochitiramo maseŵera olimbitsa thupi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena