Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 1/8 tsamba 14-17
  • Kuchezera kwa Papa ku Australia—Kokha Ulendo Wachipembedzo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchezera kwa Papa ku Australia—Kokha Ulendo Wachipembedzo?
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Penya, Mvetsera, ndipo Kenaka Weruza”
  • “Kupukuta Manja Awo Pamaso pa Papa”
  • Ndani Analipira Mtengo?
  • Chigwirizano—Pa Nthaŵi Za Yani?
  • “Mwinamwake Akufunikira Wolemba Mawu Watsopano”
  • “Tchalitchi Chitambasula Mikono Yake kwa Inu”
  • Uthenga wa Anthu a ku Australia
  • Zotulukapo Zina Zamuyaya?
  • Ulendo wa Papa ku UN Kodi Unakwaniritsanji?
    Galamukani!—1996
Galamukani!—1988
g88 1/8 tsamba 14-17

Kuchezera kwa Papa ku Australia—Kokha Ulendo Wachipembedzo?

Ndi Mlembi wa “Galamukani!” mu Australia

PA LOLEMBA, November 24, 1986, ndege ya Air New Zealand Boeing 767 inatera pa Canberra, mzinda waukulu wa Australia. Mu ndegemo munali Papa John Paul II, akuchezera kontinenti yaing’ono koposa m’dziko monga mbali ya ulendo wake wa kumaiko akutsidya la nyanja.

Akumupatsa moni anali bwanamkubwa wamkulu ndi nduna yaikulu ya Boma ya ku Australia, limodzi ndi akazi awo, ndiponso, ndithudi, anthu ambiri olemekezeka a Tchalitchi cha Roma Katolika, pakuti uwu unali ulendo wa mmodzi amene sali kokha mtsogoleri wa chipembedzo komanso mkulu wa dziko.

Malonje atatha, John Paul analunjikitsa nkhani yake yotsegulira kwa nzika zonse za mu Australia, osati kokha kwa Aroma Katolika. Anayamba kunena kuti: “Kwa nzika zonse za mu Australia, anthu abwino osakaikiritsa, Ndabwera monga bwenzi . . . Ndikufungata dziko lonse: achichepere ndi achikulire, opanda mphamvu ndi amphamvu, aja omwe amakhulupirira ndi aja omwe mitima yawo iri yolemeredwa ndi kukaikira.”

Ngati “aja okhulupirira” anatanthauza Aroma Katolika, chiŵerengero mu Australia chiri chifupifupi 4 miliyoni—25 peresenti chiŵerengero cha anthu am’dziko onse. Ngakhale kuti Australia kwa nthaŵi yaitali yakhala ikulingaliridwa monga chitaganya chakudziko, chiŵerengero cha Akatolika ogwira ntchito m’dzikoli chiri chachikulu. Komabe, 35 kufika ku 38 peresenti ya Akatolika okhala mu Australia amapezeka nthaŵi zonse pa Misa.

Mosasamala kanthu za ichi, ngakhale kuli tero, Tchalitchi cha Chikatolika mu Australia chiri ndi mavuto ake. Mu ma 1950 tchalitchi chinagawanika ndi kutsutsana kwa ogwira ntchito, kutulukapo m’kukula kwa magulu a mpatuko omwe akhala mowonjezera kusulizana wina ndi mnzake. Ndiponso, anthu opezeka pa Misa akuchepera, ndipo mathayo a unsembe akuchepera. Kuwonjezerapo, owonjezereka a abusa Achikatolika akunyalanyaza ziphunzitso za tchalitchi pa kuchinjiriza kukhala ndi mimba, kuchotsa mimba, ndi kulekana mu ukwati.

“Penya, Mvetsera, ndipo Kenaka Weruza”

Mutu wosankhidwa kaamba ka kuchezera kwa papa unali wakuti “Kristu njira, chowonadi ndi moyo.” Uwu unali mutu wabwino wa m’Malemba, ndipo ambiri anayang’ana kutsogolo kwa papa kupereka chitsogozo china ndi chowonadi pamavuto amene lerolino akuyang’anizana ndi Akatolika ndi anthu a ku Australia mwachisawawa. Ena anayembekezera kuti iye angatsutse kuyesera kwa zida za nyukliya mu Pacific—vuto lomwe liri pakhomo penipeni pa Australia. Ena anakondweretsedwa kudzamva iye akuchirikiza kuyenera kwa Aboriginal kapena kulankhula za kutsutsana pa ntchito ndipo kapena mwinamwake kukambitsirana kuyenera kwa akazi.

Wopanga makonzedwe akuchezetsa, mtsogoleri wa chipembedzo wa ku Australia Brian Walsh, wansembe wotumikira kwa zaka 30, anali kuyembekezera kuti zinthu zofunika zidzakwaniritsidwa m’nkhani za papa. Chotero analimbikitsa onse ngakhale azondi, “kupenya, kumvetsera, ndipo kenaka kuweruza.”

“Kupukuta Manja Awo Pamaso pa Papa”

Papa John Paul anali atapanga maulendo a kutsidya kwa nyanja oposa 30 asanabwere ku Australia, ndipo maiko 60 ndi oposapo omwe anachezera anawona cholembedwa cha kulongosola konse chitatulutsidwa kukumbutsa nthaŵiyo ndipo mwinamwake, kupeza phindu kaamba ka anthu opititsa patsogolo. Australia sanali wosiidwako. Tchalitchi chinayesayesa kuika chinjirizo lalikulu pa zogulitsa zoterozo m’chikhulupiriro chakuti “palibe chirichonse choipa koposa mkawonekedwe [chomwe] chikutuluka.” Koma iyi iri nthaŵi zonse mbali yomvetsa chifundo. Mwachitsanzo, m’viringo wodziŵika kwambiri wa Chikatolika anadandaula pa nsalu zopukutira mbale zachikumbukiro ndi anthu “akupukuta manja awo pa nkhope ya papa” M’virigo m’modzimodziyo ananenanso kuti: “Talingalirani Ulaliki wa Pa Phiri ukuperekedwa, wozunguliridwa ndi anthu ogulitsa zinthu zachikumbutso, anthu ogulitsa mkate wokhala ndi nyama pakati, makamera a TV ndi Portaloos [zimbudzi zokhoza kunyamula].”

Komabe, siunali unyinji wa ma medulo okongola, masipuni, ma T-shirt, ndi zikwangwani zomwe zinakoka ndemanga yaikulu. Chinali chithandizo chonse. Wothandiza m’modzi anali wophika mowa yemwe anapereka zitini za mowa zokhala ndi chisoti chachifumu cha papa. Pakuti anthu a ku Australia ali pakati pa anthu amene amamwa mowa mopambanitsa m’dziko, kachitidweko kanatsimikizira kukhala kopindulitsa. Komanso kanapangitsa mkangano ndi kusuliza konkitsa.

Wothandiza wina anali wa ku kampani ya migodi mu Australia yomwe iri yodziŵika kwambiri kaamba ka kutsutsa kwakukulu malamulo a Aboriginal, nkhani yomwe papa anadziŵika kuichirikiza mwamphamvu. Chotero sichinali chodabwitsa kuti kuvomereza kaamba ka thandizoli kunadziŵika kukhala kwachilendo. Ndithudi, ena anali kulankhula mwamphamvu ponena za nchifukwa ninji panali chifuno kaamba ka thandizo nkomwe. M’virigo wina anatulutsa kutsutsa kwake mwakunena kuti: “Ngati Yesu akanabwera, palibe aliyense akanamuthandiza iye. Angathire nkhondo pa lingaliro lonse la thandizo logwirizana.”

Ndani Analipira Mtengo?

Ngakhale kuti kuitanidwa kwambiri kunachokera ku Tchalitchi cha Chikatolika, chikuwoneka kuti wansembe wamkuluyo amachezera kokha ku maiko kumene chiitano chinalandiridwa kuchokera ku boma kapena kwa mkulu wa dziko. Ichi chinatanthauza kuti kaamba ka kuchezera kwa Australia, ponse paŵiri boma la atsamunda ndi la dzikolo anagawana mbali ya zotaika.

Anthu ena amene sali a Katolika anamva lingaliro la kusoweka kwa chilungamo pa kufunsidwa kugawana m’kulipira mtengo, makamaka popeza ena anakhulupirira kuti ulendo waposachedwapa wa Archbishop wa ku Canterbury unachitika osadziŵika. Chosokoneza kwambiri kwa ena chinali chakuti ndalama zowonongedwa zinayerekezedwa kuwirikiza nthaŵi 12 pa ndalama zomwe zinawonongedwa pa kuchezera koyamba kwa Mfumukazi Elizabeth II.

Chigwirizano—Pa Nthaŵi Za Yani?

M’kuyesayesa kubweretsa chigwirizano cha Chikristu ku kuchezerako, ngakhale kuli tero, papa analankhula kwa oimira osonkhana a magulu ena a zipembedzo 14 mu Melbourne ndipo anachita utumiki wa kusakaniza zipembedzo kumeneko, kulimbikitsa onse kuika pambali kusiyana kwawo ndi kupemphera kaamba ka mtendere. Anachezera St. Paul’s Anglican Cathedral mu Melbourne, ananena pemphero kaamba ka mtendere, ndipo anayatsa kandulo yophiphiritsira chiyembekezo cha kugwirizanaso kwa matchalitchi Achikristu.

Kulankhula mwachisawawa, anthu a ku Australia achiProtestanti anali aulemu ndipo a mkhalidwe wabwino mkati mwa nthaŵi imene wansembe wamkulu anali m’dzikomo. Koma zipembedzo zina, monga ngati Anglican, Presbyterian, ndi a Baptist, anachipanga icho kumvekera bwino kuti iwo sanavomereze papa monga mkulu wa Akristu onse kapena kunena kuti mtumwi Petro anali bishopu mu Roma. Anagogomezera kuti kudzinenera kotero sikunapeze chichirikizo m’Malemba kapena m’mbiri ya tchalitchi. Ku mbali ina, tchalitchi cha Uniting, chomwe chiri ndi atsatiri ambiri mu Australia, chinalandira kuchezerako, chikumanena kuti mwa anthu ambiri m’tchalitchi chawo, papa anali m’njira ina papa wawonso.

“Mwinamwake Akufunikira Wolemba Mawu Watsopano”

Mwachiwonekere, mawu onse a papa analembedwa mu Australia ndi kutumizidwa ku Roma, kumene papa iyemwini analemba iwo mu chiPolishi, kuwonjezera nsonga ziri zonse zomwe anapeza kuti ziri zofunika. Winawake anatembenuzanso mu Chingelezi, ndipo bishopu wa ku Australia anaika chisamaliro pa chotulutsidwa chomaliziracho. Papa kenaka anayesa mawu omwe adzalankhula pamaso pa mkulu wa phwando la mkulu wansembe, yemwe ali mwamuna wa ku Ireland.

Olemba omwe amakhala m’nyumba ya papa achidziŵitso akhala kwa nthaŵi zambiri akumva zambiri zomwe papa adzanena m’nkhani yake yokonzekeredwa. Komabe, chinenero chopatsidwa dzina lakuti papalese chingakhale chovuta kumvetsetsa, ngakhale kwa amtola nkhani achidziŵitso. Wolankhula nkhani mmodzi wochokera ku Italian news agency analingalira kuti nkhani za papa kaŵirikaŵiri zinali zovuta kumvetsetsa ndipo zazitali. Mtola nkhani wa ku Australia anasonyeza kukhumudwitsidwa kuti nkhani za chipembedzo zinali zofewa m’kalankhulidwe ndipo zodzazidwa ndi kudzizindikiritsa kwaumwini m’nkhani zowona. Wolemba nkhani za mu nyuzipepala wina, akulemba mu nyuzipepala ya Sunday Telegraph, anati: “Nkhani zake zinali zosasintha, kaŵirikaŵiri akumanena zinthu zodziwikiratu, ndipo nthaŵi zina zinthu zovuta kuzimvetsetsa . . . Mwinamwake akufunikira wolemba mawu watsopano . . . Ngati nkhani zake zimasokoneza olemba nkhani izo zingasokonezenso kotheratu anthu wamba omwe akufuna chiwunikiro.”

“Tchalitchi Chitambasula Mikono Yake kwa Inu”

Mosasamala kanthu za chisokonezo chonenedwa ndi alembi ena, ngakhale kuli tero, tchalitchi chinayembekezera kuti nkhanizo sizidzasokoneza kotheratu anthu wamba omwe akufuna chiwunikiro. Anthu ambiri analimbikitsidwa ‘kubwera, kupenya, ndi kumvetsera,’ ndipo anabweradi zikwi zikwi. Chiŵerengero chapamwamba cha opezekapo pa malo amodzi ena chinalingaliridwa kukhala nusu ya theka ya miliyoni pa Sydney Randwick Racecourse. Pa ulaliki wake kumeneko, John Paul anaika chisamaliro choyamba pa aja omwe anawonedwa monga Akatolika opanduka. Ndi mikono yake yotambasuka pa jesicha yofutukuka, iye anachonderera: “Kwa onse omwe achoka ku nyumba yawo yauzimu ndifuna kunena kuti, Bwererani! Tchalitchi chitambasula mikono yake kwa inu, Tchalitchi chikukondani inu.”

Mwakuthupi, unalidi ulendo wotopetsa kwa munthu wa zaka 66 zakubadwa. Zonse pamodzi, papa anayenda kwa mamailosi 6,800 (11,000 km) mkati mwa chifupifupi mlungu umodzi ndipo anapezeka pa zochitika zosiyanasiyana 50, kuphatikizapo phwando la Mgonero (Misa) m’mizinda yaikulu ya dziko, limodzinso ndi mu Darwin ndi Alice Springs. Kwa okhulupirira ambiri, chinali chokumana nacho chozama m’malingaliro. Mwamuna mmodzi mu Western Australia anachitira ndemanga kuti: “Pamene papa anafika [mu Perth] chinali monga kulowa kwa Kristu ku Yerusalemu.” Wina wake mu Melbourne anachitira ndemanga ponena za kupezekapo kwake: “Ali ndi chinenero cha thupi chowonedwa m’kaphunzitsidwe kachinsinsi ka ku India.” Ambiri anafuula mwapoyera.

Okonza makonzedwe akuchezera anali mwachisawawa okhutiritsidwa ndi unyinji waukulu wa opezekapo pa misonkhanoyo. Ambiri a awo omwe anapezekapo anasangalala kuwona magulu oimba nyimbo za rock 14, oimba ophunzitsidwa bwino, chandamali cha mizinga 21 cha kuchingamira, akalinde a papa, magalimoto oyenda bwino mu mzera, ndi mbendera. Kunali ngakhale anthu ochita zinthu zoseketsa, onenedwa kuti anakonzekeretsedwa “kuika kumwetulira pamaso pa anthu.”

Wansembe wa Chikatolika, amene alinso mmodzi wa olemba nkhani mu danga la nyuzipepala ya Sydney Telegraph, analemba kuti: “Chotero, umu ndi mmene papa woyenda pa ulendo wa chipembedzo akubwerera kudzakumana ndi anthu a ku Australia: anthu osakhala Akatolika ndi Akatolika m’piringupiringu wa anthu otanganitsidwa, m’chiwonetsero cha pamsewu chotenga madola mamiliyoni ambiri.” “Papa anabwera monga woyenda pa ulendo wa chipembedzo ndi kuzizwitsa konse ndi piringupiringu wamkulu wa anthu.” Mkonzi wa Sydney Morning Herald anachitira ndemanga za chimene chinawonekera kukhala chigogomezero pa ngodya ya “chiwonetsero”: “Ndipo iri ndi seŵero lomwe papa woyenda pa ulendo wachipembedzo akulitenga. Chiwonetserocho, chinawoneka kuti, chidzakhala uthenga . . . Funso lovutitsa maganizo liri lakuti: ndi kwa utali wotani kumene chisonkhezerocho chidzakhalira?”

Uthenga wa Anthu a ku Australia

Kwa zikwi zomwe zinabwera kudzamvetsera, ndi uthenga wotani umene nkhani (zokonzedwa mu Australia) unali nawo?

Kwa Opunduka: Malire akuthupi angasinthidwe ndi chikondi cha Kristu mu chinthu chinachake chabwino ndi chokongola ndipo chingapange winawake kukhala woyeneretsedwa ndi chinthu chinachake chabwino chamtsogolo kaamba ka chimene wina analengedwera.

Pa Kusowa Ntchito: Chifuno chiri kaamba ka dongosolo la mayanjano kuzindikira kuti anthu ali ofunika kwambiri kupambana zinthu. Anthu ayenera kukumbukira nthaŵi zonse kuti wantchito ali wofunika kwambiri kupambana mapindu kapena makina.

Kwa ofalitsa nkhani: Ayenera kuzindikira kuti thayo lomwe ali nalo siliri kokha kuchitira ripoti pa choipa koma kuthandiza kuchichotsa icho, chitokoso osati kokha cha kuchitira ripoti zinthu zabwino komanso kulimbikitsa izo.

Kwa ma Aboriginal: Chimene chachitidwa sichingasinthidwenso. Malo omwe anasungidwira ma Aboriginal adakalipo lerolino ndipo amangofunikira malo abwino ndi oyenera omwe sanafikiritsidwe mpaka pano.

John Paul analankhulanso kufunika kwa mtendere pamene Chaka cha Mtendere wa Mitundu yonse cha 1986 chinasendera kumapeto ake. Akulankhula kwa khamu la anthu oposa pa 30,000 lokhala ndi achichepere ochuluka pa Phwando la Achichepere mu Sydney, wansembe wamkuluyo ananena kuti: “Ngati mufuna mtendere, gwirani ntchito kaamba ka chilungamo, . . . chinjirizani moyo, . . . lengezani chowonadi, . . . chitirani ena monga momwe mungafune kuti ena akuchitireni.”

M’nkhani yake yomaliza, analimbikitsa anthu a ku Australia kukumbukira iwo amene anali ndi kumene anali kupita, ndi kuwauza kuti monga mtundu anaitanidwa kwakukulu. Kenaka, ku kumvekera pang’ono kwa nyimbo za “Mulungu Adalitse Australia” ndi “Pa msewu ku Gundagai,” John Paul II anakwera pa masitepi a Qantas jet yonyezimira yomwe inauluka kuyenda kubwerera ku Roma kudzera ku Zisumbu za Seychelles.

Zotulukapo Zina Zamuyaya?

Ndi ziti zomwe zinali zotulukapo za kuchezera kwa papa? Brisbane Courier Mail inabwera ku mapeto otokosa maganizo awa: “Unali ulendo wa nsonga zokulira ndi zochepera, zodabwitsa ndi zogwiritsa mwala . . . Tchalitchi cha Katolika cha ku Australia chidzafunikira kulingalira kwamphamvu. Ngati Papa John Paul II, mwamuna wamphamvu yozizwitsa, sangabwezere Akatolika mkati mwa malinga a tchalitchi chikuwoneka chosalingalirika kuti chirichonse choperekedwa ndi mabishopo ake akumaloko chidzapambana.”

[Mawu Otsindika patsamba 15]

“Ngati Yesu akanabwera, palibe aliyense akanamuthandiza Iye”

[Mawu Otsindika patsamba 16]

“Papa anabwera monga woyenda pa ulendo wa chipembedzo ndi ku zizwitsa konse ndi piringupiringu waukulu wa anthu”

[Mawu Otsindika patsamba 17]

Amuna a chiAboriginal anandandama pa mzere kuti apsyopsyone dzanja la Papa John Paul II

[Mawu a Chithunzi]

Reuters/Bettmann Newsphotos

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena