Mtengo wa Kupita Patsogolo
“NDI zida zankhondo zoipa zomwe munthu ali nazo kale, mtundu wa anthu uli m’tsoka lotcheredwa msampha m’dziko iri ndi anyamata ake amakhalidwe. Chidziŵitso chathu cha sayansi chachotsa kale kuthekera kwathu kwa kulilamulira. Tiri ndi amuna ambiri a sayansi, amuna ochepa kwambiri a Mulungu,” ananena tero Kazembe Omar N. Bradley mu 1948. Anapitiriza kuti: “Munthu akudzandira mwakhungu mu mdima wauzimu pamene akuseŵera ndi zinsinsi zosadziŵika za moyo ndi imfa. Dziko lapeza kuwunika popanda nzeru, mphamvu yopanda chikumbumtima.”
Lerolino, chifupifupi zaka 40 pambuyo pake, mawu ake ali ndi tanthauzo lokulirapo. Lingalirani ichi: Ngati kupita patsogolo kwa zana la 20 kunapimidwa mu madola owonongedwa pa zida, 1986 chingakhale chaka chopambana. Kuyerekezera kwa chifupifupi $900 biliyoni zinawonongedwa ndi mitundu pa dziko lonse pa zida za nkhondo. Icho chimatanthauza “kupanga mbiri kwa $1.7 miliyoni pa mphindi . . . ndipo chimaimira chifupifupi 6 peresenti ya zopangidwa zonse za dziko,” ikusimba tero The Washington Post pa phunziro lodziimira pa lokha lopangidwa ndi Ruth Leger Sivard. Worldwatch Institute inadziŵa kuti ndalama zowonongedwa pa zida zaika “mfuti patsogolo pa mkate mu zamalonda za dziko” ndipo inawonjezera kuti chifupifupi anthu a sayansi 500,000 m’dziko lonse odzipereka ku kufufuza kwa zida anapambana “ndalama zosakanizidwa zowonongedwa pa kukulitsa zopangapanga za mphamvu zatsopano, kuwongolera umoyo wa munthu, kuchulukitsa zinthu zolimira ndi kulamulira kuipitsa kwa dziko.” Mosangalatsa, ndalama zowonongedwa pa zida za nkhondo ndi mphamvu zazikulu zatulutsa zida zokwanira kupha anthu awo mwinamwake kuwirikiza nthaŵi khumi ndi kuposapo.
Mwachiwonekere, kuwunjika kwa zida sikunachotse matenda ambiri omwe akuvutitsa mtundu wa anthu, ndiponso sizinabweretse munthu kufupi ndi mtendere. M’malo mwake, monga mmene Kazembe Bradley analongosolera zaka zapitazo: “Timadziŵa zambiri ponena za nkhondo kuposa mmene timadziŵira ponena za mtendere, zambiri ponena za kupha kupambana zomwe timadziŵa ponena za kukhala ndi moyo. Uku ndi kudzinenera kwathu kwa zana la 20 kwa kusiyanitsa ndi kupita patsogolo.”