Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 2/8 tsamba 29
  • Kuchokera kwa Aŵerengi Athu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchokera kwa Aŵerengi Athu
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kubala Kapena Kuchotsa Mimba?
  • Maphunziro a pa Koleji?
  • Mapindu a Kuŵerenga Galamukani!
  • Dziko Lapansi Chiyambire 1914
  • Maphunziro Owonjezereka Kapena Ayi?
    Galamukani!—1994
  • Zimene Tingachite Kuti Tisamapanikizike Kwambiri
    Galamukani!—2010
  • Kodi Ndingatani Ndi Vuto la Kupanikizika Kusukulu?
    Galamukani!—2008
  • Makolo—kodi Ana Anu Mukuwafunira Tsogolo Lotani?
    Nsanja ya Olonda—2005
Galamukani!—1988
g88 2/8 tsamba 29

Kuchokera kwa Aŵerengi Athu

Kubala Kapena Kuchotsa Mimba?

Pa zaka 20, wokwatiwa kale ndipo mayi wa mwana wamwamuna wa zaka zitatu za kubadwa, kunatsala pang’ono kuti ndichotse mimba. Ndiri wachisangalalo kuti sindinatero. Ndinapulumutsidwa ku chisoni chochuluka chimene mwinamwake ndikanakhala nacho. Lerolino ana anga amuna aŵiri, a zaka za kubadwa zisanu ndi zinayi ndi zisanu ndi chimodzi, ali onse aŵiri aŵerengi a magazini yanu. Pitirizanibe kufalitsa nkhani zabwino zonga izi. (August 8, 1987) Mwinamwake chidzathandiza akazi ena kusachotsa mimba.

E. B., Federal Republic of Germany

Maphunziro a pa Koleji?

Pamene ndinaŵerenga choyamba nkhani yanu yakuti “Maphunziro a pa Koleji—Kukonzekera Kaamba ka Chiyani?” ndinalingalira kwa inemwini: ‘Kulefula kwina kaamba ka maphunziro a ku koleji.’ (September 8, 1987) Koma pambuyo pa kulingalira kosamalitsa, tsopano popeza kuti ndatsiriza koleji, ndingayamikire mowonadi uphungu woperekedwa. Ngakhale kuti chiri kuchedwa kwenikweni kwa ine, ndikuyembekeza kuti anthu achichepere omwe anaŵerenga nkhaniyo azindikira kuti maphunziro a pa koleji amakukonzekeretsani inu ndithudi kaamba ka chinthu chosawoneka nkomwe. Ndimayang’ana kumbuyo ndi kumvera chisoni zaka zimenezo za moyo wanga.

S. B., United States

Mapindu a Kuŵerenga Galamukani!

Ndimayamikira kwenikweni kuŵerenga magazini yanu. Zamkati zake ziridi zakudya kaamba ka malingaliro. Iyo imachita ndi nkhani zovuta zosiyanasiyana m’njira yopepuka, njira yogomeka, kuzipangitsa izo kukhala zopepuka kaamba ka onse kuzimvetsetsa. Ndiponso, malangizo operekedwa ali ogwira ntchito ndipo osagulidwa pamtengo waukulu. Ine mwaumwini ndazipeza nthaŵi zonse kukhala zoyenera kuzitsatira. Ndimayamikira magazini yanu kwa anthu achichepere omwe akuphunzira chinenero chachilendo. Ndingapereke malingaliro akuti alembetse ku magaziniyi mu chiFrench ndi chinenero chimene iwo akuphunzira. Mwanjirayi adzakhala ndi nkhani zosankhidwa zotembenuzidwa mosamalitsa.

R. M., France

Dziko Lapansi Chiyambire 1914

Ndikuthokozani kaamba ka mpambo wa nkhani zanu pa “Dziko Lapansi Chiyambire 1914.” (August 8, 1987 mpaka March 8, 1988) Ku sukulu nthaŵi zonse tinali kuphunzitsidwa mbiri yakale kuyambira pa nthaŵi ya William the Conqueror koma osati zochitika m’dziko zaposachedwa. Ndinali ndisanamvetsetsepo nkomwe zifukwa ndi zochitika kumbuyo kwa Nkhondo ya Dziko II, yomwe inachitika m’zaka zoyambirira za ubwana wanga. “Mantha” amene munawalemba anali enieni ndipo anamvedwa ngakhale ndi ana achichepere.

C. L., England

Mpambo wa nkhani zanu za “Dziko Lapansi Chiyambire 1914” unali wosangalatsa koposa! Pamene ndinali kuŵerenga magazini yomwe inali ndi Gawo I, inali nkhani imene siinakoke chidwi changa mpang’ono pomwe, koma pamene ndinalingalira za kuiŵerenga iyo, ndinalephera kuisiya ndipo ndinapitiriza kuŵerenga Gawo II, lomwe ndinali nalo, ndikumalira kuti ziŵerengero zotsatira zinali kudakalibe. Ndi kalelonse ndinali ndisanakhalepo ndi chikondwerero chotero m’zochitika za m’zaka zapita.

J. E. S. J., Brazil

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena