Kuipa ndi Kuvutika—Kodi Izo Zidzatha Motani?
ZOKUMANA NAZO zoipa kaŵirikaŵiri zimakalipitsa. Bwanji, ngakhale kuli tero, ngati pali chifukwa chenicheni kaamba ka kuvutika kwa anthu? Ndi chimenecho m’malingaliro, tiyeni tipitirizebe ndi cholembedwa chonena za Yobu. Pambuyo pa kutha kwa kukangana kokalipitsa kutatu, mwamuna wachichepere wotchedwa Elihu ayamba kulankhula. Iye akunena kwa Yobu kuti: “Umo mukuti, ‘Chilungamo changa chiposa cha Mulungu.’” Inde, Yobu anali wodzidalira ndi wodzilungamitsa mwini. “Tawonani!” akutero Elihu. “Ndidzakuyankhani mmene muli mosalungama; pakuti Mulungu ndiye wamkulu woposa munthu.”—Yobu 35:2; 33:8-12.
Mulungu wasiya umboni wokulira wakuti iye ali wabwino. (Machitidwe 14:17; Aroma 1:20) Chotero kodi kukhalapo kwa kuipa kuli chinthu chirichonse cha kutokosera ubwino wa Mulungu? Elihu akuyankha: “Nkutali ndi Mulungu kuchita choipa, ndi wamphamvuyonse kuchita chosalungama!”—Yobu 34:10.
Mulungu—Wopanda Mphamvu Molimbana ndi Kuipa?
Chotero, kodi chingakhale kuti, Mulungu anali kokha wopanda mphamvu zokwanira kulowereramo mokomera Yobu kapena wina aliyense? Kutalitali! Ndi kuwomba kwa mphepo yowopsya, Mulungu tsopano akulankhula kaamba ka iyemwini, akumazindikiritsa molimba kukhala kwake wamphamvuyonse. “Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi?” Iye akufunsa tero kwa Yobu. Nkulekelanji, popeza kuti kutalitali nkukhala wokhala ndi polekezera, iye akulankhula za iyemwini monga Mmodzi yemwe angakhoze kulamulira nyanja ndi kulamulira miyamba ndi zolengedwa zake zamoyo.—Yobu 38:4, 8-10, 33; 39:9; 40:15; 41:1.
Zowona, Mulungu sakulongosola kwa Yobu chifukwa chimene iye anamlola iye kuvutika. Koma “kodi pali chikhoterero cha kupeza cholakwa ndi Wamphamvuyonse?” Mulungu akufunsa tero. “Ndithudi, kodi udzachepetsa chilungamo changa? Kodi udzanditcha ine woipa kotero kuti ukhale wolungama?” (Yobu 40:2, 8, NW) Chotero, chiri kuchita mwansontho kotani nanga, kupatsa mlandu Mulungu kaamba ka kuvutika kwa dziko kapena kuchirikiza nthanthi zopeka kaamba ka iye! Monga mmene Yobu wasonkhezeredwa kuchita tsopano, oterewa adzachita bwino “kulapa” ponena za nthanthi zawo zosuliza.—Yobu 42:6.
Nkhani Zodzathetsedwa
Yobu sanazindikire kuti kuvutika kwake kunaphatikizapo unyinji wochulukira wa nkhani zomwe zinadzutsidwa mwamsanga pambuyo pa kulengedwa kwa munthu. Panthaŵi imeneyo cholengedwa chauzimu choukira chotchedwa Satana (“Wotsutsa”) chinatsogolera munthu kukuchimwa. Mulungu analamulira Adamu ndi Hava kupewa kudya kuchokera ku “mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa.” Iwo anafunikira kulemekeza kuyenera kwa Mulungu kuti azindikire chimene chinali chabwino kapena choipa kaamba ka iwo. Wotsutsa, ngakhale kuli tero, anafesa zikaikiro m’malingaliro a Hava, akumanena kuti: “Eya! Kodi anatitu Mulungu, usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Chotsatira iye anasuliza Mulungu kuti: “Kufa simudzafa ayi; chifukwa adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu.”—Genesis 2:17; 3:1-5.
Mawu onyenga a Satana anadzutsa nkhani zodidikiza: Kodi Mulungu anali wabodza pamene analamulira imfa kaamba ka kudya chipatso choletsedwa? Ngakhale kuli tero, kodi ndi kuyenera kotani kumene iye anali nako kwa kulanda zolengedwa zake ufulu ndi kudidikiza malamulo ake pa izo? Kodi iye sanali Mulungu wadyera, akumabisa chomwe chinali chabwino ku zolengedwa zake? Kodi chingakhale chakuti ufulu kuchokera kwa Mulungu unali wofunika?
Kupha owukira kukanachita zochepera kuposa kokha kungodzutsa mafunso ochulukira. Kokha mwa kulola kudziimira pa okha kuchoka kwa Mulungu kupita osafufuzidwa kaamba ka nyengo yokwanira ya nthaŵi ndi pamene icho chikanatsimikiziridwa—kamodzi osabwerezedwanso—kuti chogawira cha Satana cha kudziimira pa okha chiri chiitano ku ngozi. Inde, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi, osati m’mphamvu ya Mulungu. (1 Yohane 5:19) Matenda, chisalungamo, ukapolo wa chuma, zoŵawitsa—zonsezi zakhala zipatso za kusankha kwa munthu kwa kudziimira pa okha kuchoka kwa Mulungu ndi kukhala pansi pa ulamuliro wa usatana! Ndipo mosasamala kanthu za kupita patsogolo kulikonse kwa zopangapanga, mikhalidwe ya dziko ikupitirizabe kuipirako—kaŵirikaŵiri chifukwa cha zopangapanga zamakono.
Kulekerera kwa Mulungu kwa zochititsa chisoni zosakhoza kuyerekezedwa, ngakhale kuli tero, sikungamupangitse iye kukhala wosalungama. Mosiyanako, kusalungama kwa munthu ‘kwadzutsa chitsimikiziro ku chilungamo cha Mulungu.’ (Aroma 3:5) Motani?
Kuvutika Kuchotsedwa—Kosatha!
“Cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano,” anatero mtumwi Paulo. (Aroma 8:22) Inde, zaka za ngozi 6,000 za kudziimira kwa munthu payekha zasonyeza mawu a Yeremiya 10:23 kukhala owona: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” Mwamsanga, ngakhale kuli tero, Mulungu adzaloŵereramo molungama ndi kuyamba kutsogoza zinthu za mtundu wa anthu.
Ndi zotulukapo zangozi za kudziimira kwa munthu payekha zitawonetsedwa kotheratu, Mulungu kenaka angakhoze kuchotsa zinthu zonse zomwe zachititsa kuvutika: “Nkhondo, matenda, upandu, chiŵaŵa—ngakhale imfa yeniyeniyo! (Masalmo 46:8, 9; Yesaya 35:5, 6; Masalmo 37:10, 11; Yohane 5:28, 29; 1 Akorinto 15:26) Chiri monga mmene mtumwi Yohane anamvetsera m’masomphenya a m’mwamba: “Mulungu . . . adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Mokondweretsa, Mulungu anathetsa kuvutika kwa Yobu mwa kubwezeretsa umoyo wake ndi chuma ndi kumdalitsa iye ndi banja lalikulu. (Yobu 42:10-17) Mofananamo, Baibulo limatilonjeza ife kuti: “Masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzawonetsedwa kwa ife . . . cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi ndi kulowa ufulu wa ulemelero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:18, 21) Chotero kuipa kudzachotsedwapo kotheratu kuchoka m’zikumbukiro zathu!—Yerekezani ndi Yesaya 65:17.
Kukhala ndi Moyo ndi Zoipa
Kufikira ufulu umenewo utadza, tifunikira kupirira kukhala ndi moyo m’dziko loipali, osayembekezera Mulungu kutichinjiriza ku ngozi zaumwini. Satana Mdyerekezi anadzutsa chiyembekezo chabodza pamene ananyenga Yesu Kristu kudumpha pa kachisi, akumapotoza lemba la Baibulo la pa Masalmo 91:10-12, limene limati: “Palibe choipa chidzakugwera, . . . pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m’njira zako zonse.” Yesu, ngakhale kuli tero, anatsutsa kulingalira kuli konse kwa kulandira chitetezero chozizwitsa cha kuthupi. (Mateyu 4:5-7) Mulungu amalonjeza kuchinjiriza kokha kukhalapo kwathu ndi moyo kwauzimu.
Chotero Akristu owona “samadandaula pa Yehova,” ngakhale ngati tsoka lakantha. (Miyambo 19:3) Popeza kuti “yense angowona zomgwera m’nthaŵi mwake” ngakhalenso Akristu. (Mlaliki 9:11) Komabe, sitiri opanda chiyembekezo. Tiri ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha m’dziko latsopano lolungama, kumene kuipa sikudzakhalakonso. Tingakhoze nthaŵi zonse kufikira Yehova Mulungu m’pemphero, popeza kuti iye amalonjeza kutipatsa ife nzeru zofunika kupirira chiyeso chirichonse! (Yakobo 1:5) Timasangalalanso ndi kuchirikiza kwa Akristu anzathu. (1 Yohane 3:17, 18) Ndipo tiri ndi chidziŵitso chakuti kukhulupirika kwathu pansi pa chiyeso kumapangitsa mtima wa Yehova kusangalala!—Miyambo 27:11.
Chikhalirechobe, kupirira choipa sikuli kopepuka. Chotero, pamene tikutonthoza wina yemwe akuvutitsidwa, chiri chabwino ‘kulira ndi iwo akulira’—ndi kupereka thandizo logwira ntchito. (Aroma 12:15) Ana, yemwe wangotchulidwa poyambirirapo, anathandizidwa kuchira ku ngoziyo. Iye ali mmodzi wa Mboni za Yehova ndipo wapeza kuti Akristu anzake anali ofunitsitsa kwambiri kuthandiza, kumpatsa iye pogona pa kanthaŵi. Ngakhale kuti iye mwa kamodzikamodzi amadzimva kukhala wopsyinjika, iye amapeza mpumulo m’chiyembekezo cha Baibulo. “Ndikudziŵa kuti ana anga adzabweranso m’chiukiriro,” akulongosola tero Ana. Chikhulupiriro chake mwa Mulungu wa ubwino chiri motero cholimba kuposa kale.
Ngati inu mukupyola m’nyengo ya kuvutika, funsani Mboni za Yehova kuti zikuthandizeni inu ndi mafunso anu ndi zikaikiro. Kuchokera kwa iwo inu mungapezenso bukhu lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lomwe liri ndi mitu yothandiza yakuti “Kodi Nchifukwa Ninji Mulungu Walola Kuipa?” ndi “Mukulowetsedwa m’Nkhani Yofunika.” Zowona, tsopano lino zinthu zoipa zimachitika kwa anthu abwino, koma posachedwapa zonsezo zidzasintha. Pezani tsatanetsatane wochulukira kaamba ka inueni mwakufufuza Mboni za Yehova pafupi nanu kapena kulembera ofalitsa a magazini ino.
[Zithunzi patsamba 9]
M’dziko latsopano lolungama la Mulungu, kuipa kudzakhala kokha zikumbukiro zozimiririka