Kuchokera kwa Aŵerengi Athu
Kukhulupirira Mizimu
Ndikufuna kuchitira ndemanga pa nkhani ya mu Galamukani! yakuti “Allan Kardec—Ngwazi ya Kukhulupirira Mizimu.” (November 8, 1987) Ndimakhulupirira kuti aliyense ali ndi kuyenera kwa kusankha chipembedzo chimene iye afuna, malinga ngati chidzutsa munthuyo kuchita chimene chiri chabwino ndipo sichivulaza anthu ena kapena zinyama. Ndine wokhulupirira mizimu, ndipo m’kalasi momwe ndimasonkhana, omwe amapezekapo samawononga nthaŵi kusuliza zipembedzo zina, kusatchula kuwononga mapepala ndi ndalama kufalitsa zisulizo zoterozo. Okhulupirira mizimu samavomerezana ndi Mboni za Yehova ponena za kusafa kwa moyo, kulankhula ndi akufa, ndi zinthu zina. Komabe, sitiri ambuli kapena opanda chikondi kunena kuti mumagwirizana ndi ziwanda, monga mmene mumachitira kwa ife. Kukhulupirira mizimu kumatidzutsa ife ku kusintha kwa aliyense, kusintha zosakhala zenizeni kukhala zenizeni. Imatilangiza ife kuchita ntchito zabwino ndi kulimbikira ndi abale athu opanda mwaŵi. Chiri chosatheka kaamba ka ziwanda kulangiza anthu kuchita mofananamo, popeza kuti sizingakhoze kutenga mwaŵi uliwonse wa kuchita tero. Pali kusiyana kochepa, kodi simulingalira tero?
C. M. G., Brazil
Tikuvomereza kuti aliyense afunikira kukhala waufulu kusankha chipembedzo chake. Komabe, timadzimva kukhala ndi thayo kubweretsa ku chisamaliro chenjezo la Baibulo la kachitidwe koipa ka zipembedzo. Awo omwe amakhulupirira m’kulankhuzana ndi akufa, Baibulo limasonyeza kuti, ali osalimba ku chisonkhezero cha machenjera, chonyenga chochitidwa ndi mizimu yoipa yomwe monyenga imasanduka anthu omwe anakhalapo ndi moyo ndipo tsopano ali akufa omwe ali opanda mphamvu kuchita chirichonse. (Onani Mlaliki 9:5, 6, 10 ndi Yesaya 8:19, 20.) Kaamba ka chifukwa ichi, Baibulo pa Levitiko 19:31 ndi Deuteronomo 18:10-12 limachenjeza molimbana ndi kachitidwe ka kukhulupirira mizimu ka mtundu uliwonse. Ponena za kudzutsa wina kwachiwonekere kochitidwa ndi kukhulupirira mizimu kwa kusintha mu zosakhala zenizeni kukhala zenizeni, Baibulo pa 2 Akorinto 11:14, 15 limanena kuti “Satana yemwe adziwonetsa ngati mngelo wa kuwunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adziwonetsa monga atumiki a chilungamo.” Monga momwe zasonyezedwera pa 2 Timoteo 3:16, 17, munthu wa Mulungu afunikira kuyang’ana ku Baibulo, osati ku mizimu, monga magwero owona, odalirika a chitsogozo chonena za chifuno cha Mulungu.—ED.
Kuipitsa
Ndinaŵerenga ndi chikondwerero nkhani zanu pa “Kodi Nkhalango Zingasungidwe?” (December 8, 1987) Ndinadabwa chifukwa chimene inu simunapereke malingaliro—chomwe chikuwoneka kwa ine kukhala chothetsera chenicheni chomwe chingakhale chosinthana ndi kuipitsa, kuchepera kwa mafuta ofukulidwa pansi—kugwiritsira ntchito kwa magwero osakhoza kutha, mphamvu zosakhala ndi polekezera, mphamvu ya dzuŵa. Iyo iri yowonekera ndipo idzapereka magwero amphamvu kosatha.
R. A. M., United States
Tiri ovomereza ponena za kuthekera kwa mphamvu ya dzuŵa kukhala monga chothetsera ponse paŵiri m’kuipitsidwa kokulira kwa dziko lapansi ndi kupatsidwa kochepera kwa mafuta a pansi panthaka. (Onani kope lathu la February 22, 1980, Chingelezi) Komabe, vuto lokulira liri lija la dyera la munthu ndi chikondwerero chapadera, chomwe chimadidikiza kakulidwe ndi kugwiritsira ntchito kwa dziko lonse kwa mphamvu ya dzuŵa. Kaamba ka zifukwa zimenezi, timakhulupirira kuti kokha Ufumu wa Mulungu udzakhala wokhoza kufikira iwo weni mokhutiritsa ku mavuto onse ophatikizidwa ndi kupereka yankho losatha.—ED.